Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • scl tsamba 62-64
  • Kuphunzira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuphunzira
  • Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
scl tsamba 62-64

Kuphunzira

N’chifukwa chiyani Mkhristu ayenera kumaphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse?

Sl 1:1-3; Miy 18:15; 1Ti 4:6; 2Ti 2:15

Onaninso Mac 17:11

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Sl 119:97-101​—Wamasalimo ananena akuti ankakonda chilamulo cha Mulungu ndipo akamamvera chilamulocho zinkamuthandiza kuti zinthu zizimuyendera bwino pa moyo wake

    • Da 9:1-3, mawu am’munsi​—Mneneri Danieli atawerenga mabuku opatulika, zinamuthandiza kudziwa kuti nthawi imene Aisiraeli angadzachoke ku ukapolo ku Babulo, inali itatsala pang’ono kutha pambuyo pa zaka 70

N’chifukwa chiyani tifunika kupitiriza kuphunzira mfundo zowonjezereka?

Ahe 6:1-3; 2Pe 3:18

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Miy 4:18​—Mofanana ndi mmene kuwala kwa m’mawa kumayambira pang’onopang’ono, munthu wauzimu amamvetsa choonadi cha m’Baibulo pang’onopang’ono Yehova akaulula choonadi kwa anthu omwe amamukonda

    • Mt 24:45-47​—Yesu analosera kuti m’masiku otsiriza adzasankha “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru,” yemwe adzatipatse chakudya chauzimu chimene chimatithandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova

N’chifukwa chiyani tiyenera kuona kuti nzeru za m’Baibulo n’zapamwamba kwambiri kuposa nzeru zopezeka m’mabuku olembedwa ndi anthu?

Mla 12:11-13; 1Ak 3:19; 1Ti 6:20, 21; 2Pe 1:19-21

Kodi Yehova amalonjeza kuti adzachita zotani kwa anthu amene amawerenga Baibulo n’cholinga choti azichita zinthu zomwe zimamusangalatsa?

Miy 2:4-6; 9:10; Yoh 6:45

Kodi tiyenera kupempherera chiyani tisanayambe kuwerenga Baibulo?

Lu 11:13; 1Ak 2:10; Yak 1:5

Onaninso Sl 119:66

N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito mokwanira chakudya chimene “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” amatipatsa?

Mt 24:45-47

Onaninso Mt 4:4; 1Ti 4:15

N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kufufuza mfundo zolondola komanso zokwanira zokhudza zimene Baibulo limaphunzitsa?

Afi 1:9, 10; Akl 1:9, 10

N’chifukwa tifunika kupeza nzeru komanso luso lomvetsa zinthu?

Miy 4:7; Mla 7:25

N’chifukwa chiyani tifunika kumawerenga pang’onopang’ono komanso kuganizira mosamala zimene tikuwerengazo?

Yos 1:8; Sl 1:2

N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mmene tingagwiritsire ntchito Mawu a Mulungu pa moyo wathu?

Aro 15:4; 1Ak 10:11; 2Ti 3:16, 17; Yak 1:22-25

N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mozama kaye mmene tingafotokozere kwa anthu ena mfundo zomwe taphunzira?

Miy 15:28; 1Pe 3:15

Kodi tingapindule bwanji ngati timaphunzira mobwerezabwereza mfundo za choonadi?

2Pe 1:13; 3:1, 2

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • De 6:6, 7; 11:18-20​—Yehova analamula anthu ake kuti azikhomereza mawu ake mumtima mwa ana awo, kutanthauza kuti aziwaphunzitsa mawuwo mobwerezabwereza

Kodi timapeza zabwino zotani ngati timakambirana Mawu a Mulungu monga banja?

Aef 6:4

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Ge 18:17-19​—Yehova ankafuna kuti Abulahamu aziphunzitsa anthu am’banja lake lonse kuti azimvera Yehova komanso kuchita zinthu zolungama

    • Sl 78:5-7​—Ku Isiraeli, makolo ankafunika kuphunzitsa ana awo zokhudza Yehova n’cholinga choti m’badwo wotsatira udzapitirize kukhulupirira Yehova

Kodi kuphunzira pamodzi monga mpingo kumatithandiza bwanji?

Ahe 10:25

Onaninso Miy 18:1

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena