Limaloza ku Mtsogolo Mowala
Mdima ndi chiweruzo ziri kaŵirikaŵiri zonenedweratu pamene dziko likuyang’anizana ndi chiopsezo chimodzi pambuyo pa chinzake. Ndi uthenga wosiyana chotani umene uli mubukhu latsopano Worldwide Security Under the “Prince of Peace!” “Pamene ndinalitsegula, kuyang’a na kosangalatsa kunawala mu maso anga,” akulemba choncho woŵe renga m’modzi. “Zifaniziro ziri mokongola zokhudza maganizo, ndipo ndi mosangalatsa chotani mmene chifaniziro chomalizira chikusonyezera dziko lonse liri pa mtendere.”
Iye akupitiriza: “Mtima wanga uli wodzaza ndi chimwemwe pa bukhu iri. Sindikanatha kungokhala tero koma mosangalala kuwerenga mbali za ilo mofuula kwa mwamuna wanga, ndipo tsopano sindingathe kuika bukhu laling’ono limeneli—lokhala ndi uthenga waukulu—pansi, koma kupitiriza kumwa kuchokera ku iro mobwerezabwereza monga mmene kungathekere mkati mwa tsiku. Ilo liri lotsitsimula kwambiri kuposa mtsinje wa madzi wozizira koposa m’phiri.”
Landirani kope lanu. K5.00 yokha.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la chikuto cholimba, la masamba 192 Worldwide Security Under the “Prince of Peace.” (Chingelezi) Ndatumiza K5. 00.