April 12 Chikumbutso“
Ndipo mmene adatenga mkate, nayamika, anaunyema, nawapatsa, nanena, ’Ichi ndi thupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu. Chitani ichi chikumbukiro changa.’ Ndipo, choteronso chikho, atatha mgonero, nanena, ’Chikho ichi ndi pangano latsopano la mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.”’—Luka 22:19, 20.
Mboni za Yehova zikukuitanani inu kukapezekapo kaamba ka kukumbukira kusunga Chikumbutso kopambana kwambiri kumeneku. Chaka chino tsiku pa kalenda yathu lomwe likugwirizana ndi tsiku limene Yesu anafa liri Sande, April 12, pambuyo pa kulowa kwa dzuwa. Mungapezekepo pa madzulo amenewo pa Nyumba ya Ufumu imene iri kufupi ndi nyumba yanu. Fufuzani ndi Mboni za Yehova za kumaloko kaamba ka nthawi yeniyeni.