Anafikira Chonulirapo Chake
Mkati mwa nkhani ya Baibulo, minisitala ananena kuti Akristu ayenera kukhazikitsa zonulirapo za umwini ndipo kenaka kukalamila kuzifikira izo. Msungwana wa zaka zinayi yemwe anamvera nkhaniyo analengeza kwa makolo ake m’mawa wotsatira kuti iye anali atakhazikitsa chonulirapo cha kumvetsera ku bukhu lonse la masamba 256 la Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo lomwe linawerengedwa mu matepi. Mayi wake akulemba:
“lye anadzikonzekeretsa iye mwini bwino lomwe ndi ntsamilo, rekoda, matepi, ndi bukhu, ndi kufunsa kuti zakudya ziperekedwe mkati mwa tsiku lonse. Osamutenga iye mosamalitsa kwenikweni, ndinavomereza, ndikumaganiza kuti iye adzatopa mu nthawi yochepa yokha. Mkati mwa m’mawa, ndinayang’ana pa iye nthawi zochulukira ndi kuwona mmene iye anali kuchitira. Patatha chifupifupi maora awiri, ndinalingalira kuti mwinamwake ndi utali wokwanira ndipo tikadamaliza m’mawa. Koma iye anali wofunitsitsa. Pambuyo pake pa masana iye anatuluka mu chipinda, akudziwongola ndipo wotopa pang’ono, koma ndi kumwetulira konyadira. Chinatenga chifupifupi maora asanu ndi limodzi, koma anafikira chonulirapo chake!
“Popeza nthawi ino anayamba sukulu, ndipo mphunzitsi wake akunena kuti iye ali muwerengi wabwino koposa yemwe sanamumverepo ndi kale lonse.”
Inu, nanunso, mungalandire matepi amenewa ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, kapena zonse ziwiri, mwakudzadza ndi kutumiza kasilipi kotsatiraka.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, alubamu la brauni vinyl lokhala ndi matepi anayi a Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. (Chingelezi) Ndatsekeramo K54. 00. [ ] Tumizani bukhu la zithunzithunzi la masamba 256, Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, kaamba ka limene ndaikamo K20. 00 [ ] Chitani cheki chimodzi kapena zonse ziwiri, ndi kupereka ndalama zoyenera.