Kodi Mwana Wanu ali ndi Sabuskripishoni Yaumwini?
KUTI AKULITSE mwa achichepere awo chikhumbo cha kuphunzira, makolo anzeru amapangitsa mabukhu abwino kukhalapo kwa iwo nthaŵi zonse. Ambiri, mwachitsanzo, amawona ku icho kuti ana awo ali ndi sabuskripishoni yaumwini ku magazini ya Baibulo ya Nsanja ya Olonda, yomwe imagwiritsiridwa ntchito monga maziko akukambitsirana Baibulo kwa mlungu ndi mlungu pa misonkhano ya Mboni za Yehova. Koma kodi ndi pa msinkhu wotani pamene mwana ayenera kupatsidwa sabuskripishoni yaumwini?
Kumayambiriro kwa chaka chino, kalata yotsatirayi inalandiridwa kuchokera kwa mayi: “Sabuskripishoni iyi ndi ya mwana wathu wamwamuna wa zaka ziŵiri. Mkati mwa Phunziro la Nsanja ya Olonda, iye ayenera kukhala ndi kope lake lake. Ndinayesa kum’patsa iye kope lina pamene tinalibe kope lapadera, koma iye anazindikira kuti zithunzithunzi sizinagwirizane, ndipo anafuna kope limene tinali kugwiritsira ntchito. Ndiri wotsimikizira kuti zithunzithunzi zamtundu wokongola zimasangalatsa ngakhale mwana wachichepere ndipo zidzathandiza kuyamikira kwake kwa mwamsanga kwa chakudya chauzimu chimene iye sangakhale akuchimvetsetsa panthaŵiyo.”
Bwanji osatsimikizira kuti aliyense wa ana anu ali ndi sabuskripishoni yaumwini ya Nsanja ya Olonda? Landirani sabuskripishoni ya chaka chimodzi mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka, limodzi ndi K32.00.
Chonde tumizani Nsanja ya Olonda. Ndatsekeramo K32.00.