‘Monga Mkate ndi Madzi ku Mtima’
Mmenemo ndi mmene minisitala wa chiProtestanti wochokera ku Málaga, Spain, ananenera kuti magazini ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ali kwa iye. Iye analongosola kuti:
“Ndakhala pasitala wa chiProtestanti kwa zaka zambiri, ndipo ndingakutsimikizireni kuti m’maphunziro anga onse a za umulungu, sindinapeze kufupikitsidwa ndi kumvekera kumene zofalitsidwa zanu ziri nako. Kwa ine, Mboni za Yehova ali anthu osiririka; m’dziko lonyenga, iwo amakhala ndi moyo mogwirizana ndi zimene amakhulupirira. . . .
“Panthaŵi ino, chifukwa cha mavuto aumwini, sindingaphunzire ndi inu monga mmene ndingafunire kutero, koma ndithokoza Mulungu kuti, ndimalandira magazini anu, ndipo iwo ali ‘mkate’ ndi ‘madzi’ ku mtima wanga, womwe uli ndi njala ndi ludzu kaamba ka Mulungu wa moyo.”
Inu, nanunso, mungakhale nayo Nsanja ya Olonda ndi magazini inzake ya Galamukani! zikuperekedwa kunyumba kwanu mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Chonde tumizani kulembetsa kwa chaka chimodzi kwa Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ndatsekeramo K48.00.