“Iri ndi yankho ku pempho la mphunzitsi!”
Mkulu wa dipartimenti pa sukulu mu Durban, South Africa, ananena kuti iye amaŵerenga Galamukani! mokhazikika. Chifukwa cha phindu lophunzitsa la magaziniyo pa nkhani zambiri, iye anafunsa ngati angapeze chopereka cha chaka chonse. Pamene volyumu yaikulu ya Galamukani! (Chingelezi) inabweretsedwa kwa iye, iye anafuula: “Iri ndi yankho ku pempho la mphunzitsi! Ndidzauza aphunzitsi anzanga onse kuti ichi ndi chimene aliyense wa iwo ayenera kukhala nacho mu laibulale yake.”
Mwamunayo anapempha kuti pamapeto a chaka chirichonse, volyumu yaikulu ya magaziniyo idzibweretsedwa kwa iye. Pamene anauzidwa kuti mavolyumuwo anali K40.00, iye anafuula kuti: “Umenewo ndi mtengo wabwino kwambiri kaamba ka nkhani zosangalatsa zomwe ziri muno! Izo zochita ndi ana ndi mmene mungalankhulire ndi iwo ziri zothandiza koposa. M’chenicheni, nkhani zonse ziri zopereka chidziŵitso ndipo zosangalatsa kuziŵerenga.”
Volyumu yaikulu ya 1987 ya Galamukani! (Chingelezi) iripo tsopano, limodzinso ndi volyumu yaikulu ya Nsanja ya Olonda, (Chingelezi) magazini inzake ya Galamukani! Landirani mavolyumu anu mwakudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Chongani bokosi limodzi kapena onse aŵiri, ndi kutumiza chopereka chokwanira.
[ ] Chonde tumizani volyumu yaikulu ya 1987 ya Galamukani! (Chingelezi) Ndatsekeramo K40.00 (Zambia).
[ ] Chonde tumizani volyumu yaikulu ya 1987 ya Nsanja ya Olonda (Chingelezi). Ndatsekeramo K40.00 (Zambia).