Kuletsa Ana Kupita ku Misonkhano?
‘MAKANDA ndi ana sayenera kubweretsedwa m’nyumba ya Mulungu.’ Amenewo anali malingaliro a wochitira ndemanga wa Baibulo wolemekezedwa Adam Clarke. Iye, ndithudi, anapanga chivomerezo kaamba ka amayi auphaŵi omwe analibe ‘munthu wosamalira mwana wake pamene iye kunalibe.’ Oterowo angaloledwe kubweretsa ana awo ku tchalitchi “ngakhale kuti icho chidzakhala chosokoneza ku mpingo, ndi kwa atumiki ena, kumva mwana akulira.”
Clarke anazika kutsutsa kwake pa lemba la Baibulo la Nehemiya 8:2, limene limaŵerenga kuti: “Ndipo Ezara wansembe anabwera nacho chilamulo pamaso pa msonkhano, ndiwo amuna ndi akazi, ndi yense wakumva ndi kuzindikira.” Komabe, kutembenuza koteroko kumatsutsana ndi mzimu wa Deuteronomo 31:12: “Sonkhanitsa anthu, amuna ndi akazi ndi ana a ang’ono . . . kuti amve ndi kuti aphunzire.”—Onaninso 2 Timoteo 3:15.
M’chiyang’aniro cha ichi, sichikuwoneka kuti m’kukonza msonkhano umenewu Nehemiya anali ndi kusaphatikizapo aliyense m’maganizo. M’malomwake, nsonga ya chiitanocho mwachiwonekere inayenera kuphatikiza awo onse okhoza “kumva ndi kuzindikira,” kuti alimbikitse kutengamo mbali kotheratu! Chikakhala kusalingalira kotani nanga kufunsa makolo omwe ali ndi ana kuwasiya iwo popanda wowasamalira!
Mosangalatsa, Mboni za Yehova lerolino zimalimbikitsidwa kubweretsa makanda awo ndi ana ku misonkhano ya Chikristu. Zowona, panthaŵi zina ichi chingapangitse kusokonezeka kochepera ndiponso unyinji wina wa chitsenderezo pa makolo. Koma makolo Achikristu amaika patsogolo kuyesetsa kulikonse kuphunzitsa ana awo kukhala chete. M’kupita kwanthaŵi achichepere awo adzakhala “akumva ndi kuzindikira” ndipo adzatenga chidziŵitso chopatsa moyo.—Ahebri 10:24, 25.