“Sindirinso Wosakhulupirira mwa Mulungu!”
“Ndinakumana ndi mkazi wochokera ku Poland yemwe ali profesala,” akusimba tero m’mishonale mu Senegal, Africa. “Tinali ndi kukambitsirana kwakutali, ndipo ndinakalamira kuyankha mafunso ake ambiri.” Profesalayo anakana chofalitsidwa chokonzekeretsedwa kaamba ka phunziro la Baibulo, akumalongosola kuti: “Ndine wosakhulupirira mwa Mulungu. Bukhu limenelo silikundisangalatsa ine nkomwe.” Komabe, iye analandira bukhu la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation?
“Pamene ndinabwererako mlungu wotsatira,” m’mishonaleyo akusimba, “iye mosangalatsidwa anandiuza ine kuti anaŵerenga bukhulo kuchokera ku chikuto choyamba kufika ku chikuto chomalizira. Pamene ndinafunsa za kusanthula bukhu la Creation limodzi ndi iye, iye anayankha: ‘Koma ndiribe chifukwa cha kuphunzira bukhu limenelo tsopano! Ndaliŵerenga ilo lonse, ndipo lasintha kotheratu maganizo anga—sindirinso wosakhulupirira mwa Mulungu! Tsopano ndingakonde iwe kuphunzira limodzi nane mu bukhu lofiira lija limene unandisonyeza ine poyamba, limodzi ndi Baibulo!’”
Kodi mumadziŵa winawake yemwe ali wosakhulupirira mwa Mulungu kapena mwinamwake amakaikira chowonadi cha Baibulo? Bwanji osamutumizira mphatso yaumwini ya kope la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Mungachite tero mwakungodzaza ndi kutumiza kapepala kali pansipa, kutsekeramo kokha K20.00 limodzi ndi kapepalako.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, kope la mphatso la bukhu la masamba 256 Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? limodzinso ndi kalata yolongosola kuti iri mphatso yochokera kwa ‐‐‐‐‐‐‐‐‐‐‐‐‐‐‐ (dzina lanu). Ndatsekeramo K20.00 (Zambia).