Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 6/15 tsamba 8-9
  • Kusakhulupirira Kouma Khosi kwa Afarisi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusakhulupirira Kouma Khosi kwa Afarisi
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Afarisi Akana Dala Kukhulupirira
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Afarisi Anatsutsana ndi Munthu Amene Anali Wakhungu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Yesu Anachiritsa Munthu Amene Anabadwa Wosaona
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kuchiritsa Munthu Wosawona Chibadwire
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 6/15 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Kusakhulupirira Kouma Khosi kwa Afarisi

MAKOLO a wopemphapempha yemwe pa nthaŵi imodzi anali wakhungu akuchita mantha pamene aitanidwa ndi Afarisi. Iwo akudziŵa kuti chagamulidwapo kale kuchotsa mu sunagoge aliyense amene adzasonyeza chikhulupiriro mwa Yesu. Kudulidwa koteroko kwa mayanjano ndi ena m’mudzi kungapangitse chitsenderezo chachikulu, makamaka pa banja losauka. Chotero makolowo ali ochenjera.

“Kodi uyu ndi mwana wanu amene inu munena kuti anabadwa wosawona?” Afarisiwo akufunsa. “Ndipo apenya bwanji tsopano?”

“Tidziŵa kuti uyu ndi mwana wathu ndi kuti anabadwa wosawona,” makolowo akutsimikizira. “Koma sitidziŵa umo apenyera tsopano, kapena sitimudziŵa amene anatsegulira pamaso pake.” Ndithudi mwana wawo wawauza iwo zonse zimene zachitika, koma mochenjera makolowo akunena kuti: “Mumfunse iye. Ali wamsinkhu. Adzalankhula mwini za iye yekha.”

Chotero, Afarisiwo akuitananso mwamunayo. Panthaŵi ino iwo akuyesera kumutsekereza iye mwa kusonyeza kuti iwo asonkhanitsa umboni wopatsa mlandu motsutsana ndi Yesu. “Lemekeza Mulungu,” iwo akulamula. “Tidziŵa kuti munthuyo ali wochimwa.”

Munthu yemwe anali wakhunguyu sakukana kupatsa mlandu kwawo, akumawona kuti: “Ngati ali wochimwa, sindidziŵa.” Koma iye akuwonjezera: “Chinthu chimodzi ndichidziŵa, pokhala, ndinali wosawona, tsopano ndipenya.”

Akumayesera kupeza cholakwika mu umboni wake, Afarisiwo afunsanso: “Anakuchitira iwe chiyani? Anakutsegulira iwe maso bwanji?”

“Ndinakuuzani kale,” mwamunayo akudandaula, “ndipo simunamva. Mufuna kumvanso bwanji?” Mokwiya iye akufunsa: “Kodi inunso mufuna kukhala akuphunzira ake?”

Kuyankha kumeneku kukwiitsa Afarisiwo. “Ndiwe wophunzira wa iyeyu,” iwo akusuliza, “ife ndife akuphunzira a Mose. Tidziŵa ife kuti Mulungu analankhula ndi Mose; koma [ponena za mwamunayu, NW] sitidziŵa kumene achokera ameneyo.”

Akulongosola kudabwitsidwa, wopemphapempha wodzichepetsayo akuyankha: “Pakuti chozizwa chiri mmenemo, kuti inu simudziŵa kumene achokera, ndipo ananditsegulira maso anga.” Kodi ndi mapeto otani amene ayenera kupangidwa kuchokera ku ichi? Wopemphapemphayo akulozera ku lamulo lolandiridwa: “Tidziŵa kuti Mulungu samvera ochimwa, koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake amvera ameneyo. Kuyambira pa chiyambi sikunamveka kuti wina anatsegulira maso munthu wosawona chibadwire.” Chotero, mapetowo ayenera kukhala odziŵikiratu: “Ngati uyu sanachokera kwa Mulungu, sakadakhoza kuchita kanthu.”

Afarisi alibe yankho kaamba ka nzeru yachindunji, yomvekera imeneyi. Iwo sangathe kuyang’anizana ndi chowonadi, ndipo chotero akutonza mwamunayo: “Wobadwa iwe konse mu zoipa ndipo iwe utiphunzitsa ife kodi?” Pa chimenechi, iwo akuponya mwamunayo kunja, mwachiwonekere kumchotsa iye mu sunagoge.

Pamene Yesu adziŵa ponena za chimene chachitika, iye apeza mwamunayo ndi kunena kuti: “Kodi ukhulupirira Mwana wa munthu?”

“Ndipo ndani iye, ambuye,” wopemphapempha yemwe anali wakhunguyo akuyankha, “kuti ndimukhulupirire?”

“Walankhula ndi iwe ndi iyeyu,” Yesu akuyankha.

Mwamsanga, mwamunayo agwada pamaso pa Yesu ndi kunena kuti: “Ndikhulupirira, Ambuye.”

Yesu kenaka akulongosola: “Kudzaŵeruza ndadza ku dziko lino lapansi: Kuti iwo osapenya apenye, ndi kuti iwo akupenya akhale osawona.”

Pa chimenecho, Afarisi omwe akumvetsera afunsa: “Kodi ifenso ndife osapenya?” Ngati iwo akanadziŵa kuti anali akhungu mwa malingaliro, pakanakhala chodzikhululukira ku kutsutsa kwawo Yesu. Monga mmene Yesu akuwawuzira iwo: “Mukadakhala osawona simukadakhala nalo chimo.” Komabe, iwo mowuma khosi akulimbikira kuti iwo sali osawona ndipo safunikira chiwunikiro chauzimu. Chotero Yesu akuyang’ana: “Koma tsopano munena kuti, ‘Tipenya.’ Chimo lanu likhala.” Yohane 9:19-41.

◆ Nchifukwa ninji makolo a wopemphapempha yemwe anali wakhungu akuwopa pamene aitanidwa pamaso pa Afarisi, ndipo chotero ndimotani mmene iwo akuyankhira mochenjera?

◆ Ndimotani mmene Afarisi akuyesera kutsekereza munthu yemwe anali wakhunguyo?

◆ Ndi mtsutsano wanzeru wotani wa mwamunayo umene ukwiyitsa Afarisi?

◆ Nchifukwa ninji Afarisi alibe chodzikhululukira kaamba ka kutsutsa kwawo Yesu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena