Kuchita Ndi Mavuto a Moyo
Chaka chatha nyumba ya mphunzitsi wa pa sukulu mu Bignona, Senegal, inapsya. Pambuyo pake, nthambi ya Watch Tower Sosaite m’dziko la Kumadzulo kwa Africa limenelo inalandira kalata iyi:
“Chomwe chimandikwiyitsa ine kwambiri,” mphunzitsi wa pasukuluyo analongosola tero, “chiri chakuti m’motowo ndinataikiridwa mabukhu omwe ali a mtengo wosayerekezeka kwa ine. Maina awo amaphatikiza Your Youth—Getting the Best out of It ndi Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo? Ndingakhoze kuchita nazo bwino lomwe popanda zovala zanga ndi nyumba yanga, koma sindingakhoze kuchita nazo popanda mabukhu amenwo! Iwo ali ofunika kwambiri kwa ine kuposa zirizonse zomwe ndinazitaya. Ndikupemphani, chonde ndifikireni mwamsanga kumene kuli kothekera, ndi kundilola ine kudziŵa mmene ndingapezere kubwezeretsedwa kwa makopewa. Moyo uli wodzala ndi mavuto, ndipo timafunikira chidziŵitso choterocho kuwathetsa iwo ndi kutithandiza ife kupanga zosankha zolondola ndi kudzisunga eni moyenera.”
Ena ambiri amadzimva mofananamo ponena za zofalitsidwa ziŵiri zimenezi. M’chenicheni, oposa makope 22 miliyoni a bukhu la Youth ndi oposa makope 20 miliyoni a Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo? agawiridwa kuzungulira dziko lonse. Inu mungalandire mabukhu ofunika aŵiriwa mwakungodzaza ndi kutumiza kapepalaka limodzi ndi K16.00.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, mabukhu aŵiri a masamba 192, a chikuto cholimba Your Youth—Getting the Best out of It ndi Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo? Ndatsekeramo K16.00 (Zambia).