Chidziŵitso Chimene Chimabweretsa Mtendere wa Mkatikati
Mkazi wachichepere wa ku Ohio, U.S.A., akulemba kuti: “Ndinaleredwa m’Katolika, kupezeka pa tchalitchi cha Methodist pamene ndinali ku koleji, kupita kocheza ndi mnyamata wa Chiyuda, kenaka kukwatiŵa ndi m’Lutheran. Sindinasangalalepo ndi chirichonse cha zipembedzo zimenezi zomwe zinapitiriza ‘kusintha ndi nthaŵi.’ Ndinayamba kuŵerenga bukhu la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi, poyamba mokaikira ndipo ndikumakhumbira zithunzithunzi zokongola. Ndinamwerekera ndipo mwachimwemwe ndinaŵerenga theka lomalizira m’maora anayi.”
Mkazi ameneyo tsopano akunena kuti amayamikira Mulungu “kaamba ka chidziŵitso changa chatsopano ndi mtendere wa mkatikati.” Timadzimva kuti inunso mungapindule kuchokera ku chofalitsidwa cholimbikitsa chikhulupiriro chimenechi. Chimalongosola mwanjira yogwira ntchito chiphunzitso cha Baibulo chirichonse chodzutsa mtsutsano, kusonkhanitsa pamodzi umboni m’njira yoyenerera ndi yomveka imene yankho limakhala lowonekera kwa woŵerenga. Masamba 256 a bukhuli, a ukulu wofanana ndi magaziniyi, adzazidwa ndi zithunzithunzi zophunzitsa zoposa 150, zambiri mu mtundu wokongola. Kokha K24.00.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosantha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Ndatsekeramo K24.00.