Kumene Mdyerekezi Anachokera
“Ntchito yanga iri kwakukulukulu kusunga achichepere m’malamba awo a pampando ndi kuwasunga iwo abata,” akulongosola tero mkazi wachichepere yemwe amagwira ntchito ya pakanthaŵi monga wosungitsa bata wa m’basi ya sukulu mu South Dakota. Iye akusimba kuti:
“Mmodzi wa anyamatawo amandipatsadi ine mwapadera nthaŵi yovuta. Kungokudziŵitsani, iye ali kokha wa zaka zisanu ndi chimodzi zakubadwa, komabe pakamwa pake nthaŵi zina pangapange phokoso lalikulu. Ndinayenera kukhazikitsa thupi lake m’mpando wake ndi kukhala ndi dzanja langa liri pakamwa pake kumusunga iye kukhala wabata. Iye wakantha, kukanda, kutsina, kutemberera, ndi kukuwa. Pa tsiku loipa, iye amafunikira kumkhalira kumusungirira iye mu mpando wake.
“Lachisanu linali tsiku loipa, ndipo chifupifupi pa nthaŵi imene ndinali wozizira ziwalo kuchokera m’mapewa kupita kunsi, iye anafunsa kuti: ‘Nchifukwa ninji Mulungu anapanga Mdyerekezi?’ Panali kope la Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo m’basimo. Ndinamuwuza iye kuti bukhu limeneli likakhoza kumthandiza iye kuwona kumene Mdyerekezi anachokera. Kodi mungakhulupirire kuti taŵerenga nkhani 41 pamodzi? Ndinali pafupi kuleka wachichepere ameneyu, koma mkhalidwe wake wasintha ku mlingo wakuti iye samafuna kuchoka m’basi pamene tifika ku sukulu. Iye amafuna kuŵerenga m’nkhani zowonjezereka!”
Phunziro la chofalitsidwa chozizwitsa chimenechi latulutsa zotulukapo zofananazo ndi achichepere ena ambiri. Inu mungalandire kope la chofalitsidwa chokongola chochitiridwa chitsanzochi, cha zirembo zazikulu, cha masamba 256 mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka limodzi ndi K30.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu lalikulu la
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, kaamba ka limene ndatsekeramo K30 (Zambia).