Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi nkhani yonena za kuvomerezedwa ndi Mulungu imatanthauza kuti Akristu angalankhule kwa wina amene poyambapo analingaliridwa kukhala “tsamwali wovomerezedwa” koma pambuyo pake, chifukwa cha kuchita cholakwa, anayenera kupewedwa?
Inde, imatero. Nsanja ya Olonda ya November 15, 1988, inasonyeza chifukwa chimene chiriri cha Malemba kusintha kawonedwe kathu ka munthu wosabatizidwa yemwe amagawanamo mu utumiki wapoyera ndi Mboni za Yehova. Kalelo, munthu woteroyo anali kutchedwa “tsamwali wovomerezedwa.” Ngati iye pambuyo pake mosalapa anaswa malamulo a Mulungu, mpingowo unali kugalamutsidwa, ndipo ziwalozo chotero zinayenera kupewa kuyanjana ndi kulankhula ndi iye.
Monga mmene nkhani ya posachedwapa inasonyezera, Baibulo limafuna kuti kachitidwe ka chilango koteroko katengedwe mu nkhani ya anthu obatizidwa omwe ali ochita zolakwa osalapa. (1 Akorinto 5:11-13; 2 Yohane 9-11) Komabe, kuŵerengera kwa munthu wosabatizidwa yemwe akulondola njira yolakwa sikuli kofanana ndi kuja kwa yemwe ali wobatizidwa. (Luka 12:48) Iye sanabatizidwe ndipo chotero sanakhale wovomerezedwa m’maso mwa Mulungu, chotero kuchotsedwa sikuli koyenerera mu nkhani yake. Kwakukulukulu, iye tsopano ali munthu wa kudziko ndipo angachitiridwe mofananamo.
Chotero, bwanji, ponena za wina yemwe poyambapo anali kutchedwa “tsamwali wovomerezedwa” koma yemwe salinso woyeneretsedwa kaamba ka utumiki wapoyera chifukwa cha njira yake yolakwa? Popeza kuti iye sanachotsedwe, iye ayenera kuchitiridwa monga munthu wa kudziko amene iye ali.a Ndithudi, Nsanja ya Olonda ya November 15 inalangiza pa tsamba 19 kuti chisamaliro choyenera chiyenera kuchitidwa ndi Akristu okhulupirika. Awa amazindikira kuti munthu wosabatizidwa angakhale anagawanamo bwino lomwe m’kuchita cholakwa mosasamala kanthu za kukhala kwake ndi chidziŵitso cha ziyeneretso za Mulungu. Akristu achikulire ayenera kukhala osamalitsa ponena za kuyanjana ndi munthu woteroyo. Ngati mafunso abuka ponena za ukulu umene kugwirizana komwe kungakhalepo ndi iye, ambiri a awa angathetsedwe mwa kutsatira uphungu wa umulungu. Tingawunikire pa uphungu wonga uja wopezeka pa 1 Akorinto 15:33 ndi Miyambo 13:20 ndi kudzifunsa ife eni kuti: ‘Ndi mayanjano otani amene ndingakhale nawo moyenerera ndi munthu wa kudziko yemwe sakukhala ndi moyo ndi miyezo ya Chikristu?’ Ngati akulu awona kuti munthu wa kudziko wa mtundu umenewu akupereka chiwopsyezo chirichonse, iwo mwamseri angapereke uphungu wochenjeza kwa awo mu mpingo omwe akuwoneka kukhala ali m’ngozi.
M’kupita kwa nthaŵi, munthu wosabatizidwa yemwe anakhalapo “tsamwali wovomerezedwa” angapereke umboni woyenerera wa kulapa, ndipo iye angakhumbe kukhala ndi phunziro la Baibulo kachiŵirinso. (Machitidwe 26:20) Iye angalankhule kwa akulu a mu mpingo kumene iye tsopano akupezekako, amene, ngati chiwoneka choyenerera, adzakonzekera kaamba ka iye kukhala ndi phunziro la Baibulo. Ichi chidzagwiranso ntchito ngati mtsogolo winawake sayeneretsedwa monga wofalitsa wosabatizidwa ndipo pambuyo pake asonyeza kulapa. Kaŵirikaŵiri, iye afunikira kulankhula kwa akulu aŵiri omwe anasamalira kulakwa kwake kapena ena aŵiri amene bungwe la akulu lingasankhe kubwereramo mu nkhaniyo ngati iye anafunsira chimenecho.
Moyenerera, Nsanja ya Olonda inalongosola kuti icho chiri mwa njira inayake chosiyana mu nkhani ya makolo osamalira kaamba ka ana aang’ono m’nyumba—achichepere amene mwalamulo ali osadziimira paokha kaamba ka amene iwo ali ndi thayo kupereka chirikizo lakuthupi. (Aefeso 6:1-4) Malemba amaika pa makolo thayo la kulangiza ndi kutsogoza ana awo. Chotero makolo (kapena kholo lokhulupirira) angasankhe kutsogoza phunziro la Baibulo lamseri ndi wamng’ono wolakwayo kapena kumuphatikiza iye mu programu ya banja ya phunziro la Baibulo ndi kukambitsirana.
Pamene kuli kwakuti nkhani ya posachedwapa ya mu Nsanja ya Olonda imaitanira kaamba ka kuwongolera m’kulingalira ndi zochita zathu, iko kwachitidwa m’chigwirizano ndi Malemba omwe ali opindulitsa “kaamba ka chilangizo cha [m’chilunjiko, NW].”—2 Timoteo 3:16, 17.
◼ M’chiyang’aniro cha Tito 1:6, kodi ana a mwamuna ayenera kubatizidwa ngati mwamunayo ayenera kuyeneretsedwa kukhala mkulu mu mpingo?
Mu mutu woyamba wa Tito, mtumwi Paulo anandandalitsa ziyeneretso za amuna otumikira mona akulu a mpingo. Chimodzi chinali chakuti mbale akhale “wopanda chirema, . . . wokhala nawo ana okhulupirira.” Ichi sichingatanthauze kuti ana a mkulu ayenera kukhala onse obatizidwa, popeza kuti ena angakhale makanda. Chotero Tito 1:6 molingalirika iyenera kutanthauza kuti ana aang’ono a mwamuna ayenera kukhala obatizidwa kapena ayenera kukhala akuphunzira chowonadi cha Baibulo, kulandira ndi kugwiritsira ntchito icho ndi kumayenda kulinga ku ubatizo, pamene ali pansi pa chisamaliro cha banja. (1 Akorinto 7:14) Mkulu ayenera kumakalamira kupanga ophunzira a ana ake, iwo posakhala “osakaza kapena osamvera mawu.”b
Tingayamikire ichi bwinopo mwakuwona mmene Baibulo likugwiritsira ntchito kalongosoledwe kakuti “wokhulupirira.” Ndithudi, munthu angakhale ndi chikhulupiriro, kapena kukhulupirira, mu zinthu zambiri. (Machitidwe 26:27, 28; 2 Atesalonika 2:3, 11; Yakobo 2:19) Koma timapeza ”kukhulupirira” kukhala kogwirizanitsidwa mofala kwambiri ndi kulandira Chikristu ndi kubatizidwa. (Machitidwe 8:13; 18:8; yerekezani ndi 19:1-5.) Ubatizo umasonyeza makamaka kuti munthu ndi wokhulupirira.—Machitidwe 2:41, 44, 4:4, 32.
Ana ena achichepere a mkulu angakhale asanafikirebe pa kukhala okonzekera mwakuthupi, mwamalingaliro, kapena mwamaganizo kaamba ka ubatizo. Komabe, Tito 1:6 ikulongosola iwo monga “ana okhulupirira” ngati iwo akupita patsogolo kulinga ku ubatizo, m’chigwirizano ndi msinkhu wawo ndi mkhalidwe.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati winawake wokhala mu mkhalidwe umenewo sakuzindikira za kawonedwe kosinthidwa kameneka, chikakhala cha chifundo kumulozera iye ku nkhani za mu Nsanja ya Olonda zimenezi.
b Onaninso Nsanja ya Olonda ya February 15, 1972, (Chingelezi) tsamba 126.