Osati Kokha la Ana
Mkazi wa ku Fort Worth, Texas, akulemba kuti: “Ndinakhala ndi bukhu la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo kwa zaka zoŵerengeka. Ndinagamulapo kuyamba kuŵerenga ilo kwa mwana wanga wamwamuna wa miyeza khumi. Tsiku lirilonse ndinaŵerenga mitu iŵiri kapena itatu. Ndimadziŵa kuti iye akali wamg’ono kwambiri kumvetsetsa ilo. Ngakhale kuli tero, ndapindula mokulira kuchokera ku ilo mwaumwini. Bukhulo linakhudza mtima wanga m’njira yapadera kwambiri ndi kuzamitsa chikondi changa ndi chiyamikiro kaamba ka Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, Yesyu Kristu. Ndine wa zaka 27. Ndinalingalira kuti bukhu la Mphunzitsi Wamkuru’yo linali kokha la ana, ndipo tsopano ndidzimverera chisoni posaliŵerenga ilo pachiyambipo.”
Bukhu iri la chikuto cholimba lochitiridwa chitsanzo, la masamba 192 lidzatumizidwa kwa inu pa kokha K10. Monga chosiyanako, kaamba ka kokha K100 inu tsopano mungapeze bukhu ndi kujambulidwa kwa ilo pa matepi kaseti anayi mu album yokongola.
Santhulani bokosi loyenerera ndi kutumiza chopereka chokwanira:
[ ] Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la chikuto cholimba la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo; Ndatsekeramo K10 (Zambia).
[ ] Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, album yokongola ya vinyl ndi makaseti anayi ndi bukhu la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo. Ndatsekeramo K100 (Zambia). (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya kumaloko ya Watch Tower kaamba ka chidziŵitso.)