“Mwachimwemwe Ndikasankha Galamukani!”
Analemba motero Frank Senge mu Post-Courier ya ku Papua New Guinea. M’danga lake la mlungu ndi mlungu la July 19, 1988, Senge anafotokoza kuti:
‘Tsamba la zamkatimu la magazine a [Galamukani!] limalongosola kuti iwo amafalitsidwira ‘chidziŵitso cha banja lonse.’
“‘Amasonyeza mmene tingalakire mavuto amakono,’ ilo limatero.
“Ndipo amaterodi. Mosiyana ndi zolembedwa zambiri za matchalitchi ena kapena magazine, Galamukani! amalongosola Mulungu kudzera m’mavuto a dziko otizinga. . . .
“Mungawone kunenaku monga manenanena okopa achipembezo (Inetu sindine [Mboni]) . . . koma ngati tinati tisankhe magazine, abanja, mwachimwemwe ndikasankha Galamukani!”
Tikhulupirira kuti nanunso mudzasangalala ndi Galamukani! Iri ndi avareji ya kusindikiza ya magazine 11,250,000 kope lirilonse ndipo amafalitsidwa m’zinenero 54.
Chonde tumizani sabusikripishoni yachaka ya Galamukani! Ndatumiza K40 (Zambia) kaamba ka makope 12 a magazinewa (kope imodzi pamwezi).