Revelation—Its Grand Climax At Hand
“Bukhu limeneli [lokhala ndi mutu wapamwambawo] limasonyeza m’njira yozizwitsa chikondi chozama ndi kudera nkhaŵa zimene Mlengi wathu ali nazo kaamba ka anthu ake onse,” analemba motero muŵerengi woyamikira kuchokera ku Washington State. “Chiridi cholimbikitsa ndi chopatsa mphamvu kuŵerenga liwu lirilonse.”
Muŵerengi woyamikirayo anawonjezera kuti: “Kakhazikitsidwe ka chaputala chirichonse kali kosangalatsa. Ndimayamikira kalembedwe kodera ka mavesi olongosoledwa, limodzinso ndi zithunzi zokongola ndi matchati. Sindingathe kulongosola kudzimva komwe kuli mkati mwanga pamene ndikuŵerenga. Nthaŵi zambiri limandipangitsa kutulutsa misozi.”
Tikuganiza kuti nanunso mudzasangalatsidwa ndi kuzindikiritsa komveka, kwanzeru, kwa zirombo, chinjoka, mkazi wachigololo wamkulu, ndi zinthu zina zophiphiritsira za Chibvumbulutso. Inu mudzawona tanthauzo la tsiku lathu. Bukhu lachikuto cholimba losangalatsa limeneli, la ukulu wofanana ndi magazine ano, limapereka kulingaliridwa kwa vesi ndi vesi kwa bukhu lonse la Baibulo la Chibvumbulutso. Itanitsani ilo lerolino. Kokha K48, titalipiriratu positi.
Chonde tumizani bukhu lamasamba 320 la Revelation—Its Grand Climax At Hand! Ndatsekeramo K48 (Zambia).