‘Linathandiza Ana Athu Aakazi Kukhala Oyandikirana’
Polembera ku ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society chaka chatha, mphunzitsi wa pa sukulu ku Murewa, Zimbabwe, ananena kuti izi ndi zimene Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo linakwaniritsa. Mkaziyo analandira bukhulo kuchokera kwa mphunzitsi mnzake ndipo anasimba kuti:
“Ndinatsatira chilangizo chake pa mmene ndingapindulire koposa ndi bukhulo, choyamba ndi mwana wanga wamkazi wam’ng’ono pa onse wa zaka 8 zakubadwa ndipo kenaka ndi aŵiri ena, a misinkhu ya 16 ndi 18, omwe anali ku Sukulu ya Sekondale Yogonera kumeneko. Ndiri wosangalala kwambiri kukudziŵitsani kuti chivomerezo cha ana anga aakazi onse atatu chakhaladi cholimbikitsa. Makhalidwe awo akhala akusinthadi chiyambire nthaŵiyo kukhala abwinopo.” Mayiyo anawonjezera kuti: “Bukhulo lathandiza ana athu aakazi mwachipambano kukhala oyandikira kwa ife, makolo awo, kuposa ndi kale lonse.”
Bukhu limeneli lamasamba 256, lamasamba a ukulu wa magazine ano, lingalandiridwe mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka limodzi ndi K48.00. Nkhani za Baibulo 116 za bukhulo zimapatsa muŵerengi lingaliro la chimene Baibulo limanena. Nkhani zimenezi zimawoneka m’dongosolo la kuchitika kwa zinthuzo m’mbiri. Mudzapeza limeneli kukhaladi la thandizo pophunzira za nthaŵi pamene zinthu zinachitika m’mbiri, m’chigwirizano ndi zochitika zina. Bukhulo liri ndi zithunzithunzi zokongola ndi zirembo zazikulu.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu lachikuto cholimba lakuti Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, kaamba ka limene ndatsekera K48.00 (Zambia).