“Kabati ya Chuma cha Mafunso ndi Mayankho”
Umo ndi mmene mkazi wina wa ku Pittsburgh, Pennsylvania, anatchera bukhu lakumanja la Reasoning From the Scriptures. Iye analongosola kuti: “Posachedwapa Mboni za Yehova ziŵiri zinabwera pa nyumba panga. . . . Mmodzi wa iwo mosadziŵa anasiya (panyumba panga) bukhu la mutu wakuti Reasoning From the Scriptures. Ndiyenera kuvomereza, ndinasanthula ndi kupenda mosamalitsa bukhulo! Ndinakhala pansi ndi kuliŵerenga kwa maola angapo. Ndinasangalatsidwa koposa. . . . Bukhu limeneli linali ngati kabati ya chuma cha mafunso ndi mayankho kwa ine, ambiri amene ndadzifunsa ndekha.”
Inu mungalandire kope lanulanu la bukhu la Baibulo lopindulitsa limeneli limene lidzakupatsani mayankho ku mazana angapo a mafunso a pa nthaŵi yake. Ilo liri ndi mitu ya nkhani yaikulu yoposa 70. Yophatikizidwamo ndiyo “Abortion,” “Drugs,” “Holidays,” “Rapture,” “Reincarnation,” “Sex,” “Spiritism,” ndi ina yambiri. Ndandanda yake ya chosonyezera mitu ya nkhani ndi malemba ya masamba asanu ndi aŵiri ingakuthandizeni kupeza mayankho mofulumira.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu lachikuto cholimba, lamasamba 448 lakuti Reasoning From the Scriptures. Ndatsekeramo K24.00 (Zambia).