Olinganizidwa Kutumikira Mulungu
“Ndagwirizana ndi zipembedzo zosiyanasiyana ndi mipatuko yachipembedzo,” akulemba motero munthu wa ku Mexico. “Koma sindinawonepo gulu loterolo.” Munthuyo anali atangomaliza kumene kuŵerenga brosha lakuti Mboni za Yehova Zikuchita Chifuniro cha Mulungu Mogwirizana pa Dziko Lonse Lapansi. Iye analongosola kuti: “Chimene chimandisangalatsa kwambiri chiri kusamalitsa kumene mumakwaniritsira ntchito ya kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu kunyumba ndi nyumba, pantchito, m’khwalala, m’basi. Nkozizwitsa kupeza anthu amene amatenga kuchita chifuniro cha Mulungu mosamalitsa mu mbadwo uno wa chinyengo chachipembedzo chochuluka.”
Phunzirani zimene Mboni za Yehova zimakhulupirira, mmene zalinganizidwira, ndi mmene gulu lawo limagwirira ntchito pa dziko lonse. Tumizani kaamba ka mabrosha atatu a masamba 32 akuti Mboni za Yehova Zikuchita Chifuniro cha Mulungu Mogwirizana pa Dziko Lonse Lapansi, Jehovah’s Witnesses in the Twentieth Century ndi School and Jehovah’s Witnesses. Kokha K14.40.
□ Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, mabrosha atatu akuti Mboni za Yehova Zikuchita Chifuniro cha Mulungu Mogwirizana pa Dziko Lonse Lapansi, Jehovah’s Witnesses in the Twentieth Century, ndi School and Jehovah’s Witnesses. Ndatsekeramo K14.40.