Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 2/15 tsamba 30
  • ‘Kuchitira Umboni Chowonadi’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Kuchitira Umboni Chowonadi’
  • Nsanja ya Olonda​—1990
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 2/15 tsamba 30

‘Kuchitira Umboni Chowonadi’

KU FUNSO la Pilato lakuti, “Nanga kodi ndiwe mfumu?,” Yesu anayankha kuti: “Munena kuti ndine Mfumu. Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi chowonadi. Yense wakukhala mwa chowonadi amva mawu anga.” (Yoh. 18:37) Monga mmene Malemba amasonyezera, chowownadi chimene anachitira umboni sichinali kokha chowonadi wamba. Chinali chowonadi chofunika koposa cha zimene zinali zifuniro za Mulungu, chowonadi chozikidwa pa mfundo yeniyeni ya chifuno cha ulamuliro wa Mulungu ndi mphamvu yake ya kukwaniritsa chifuniro chimenecho. Kupyolera mwa uminisitala wake Yesu anavumbula chowonadi chimenecho, chimene chinali “m’chinsinsi chopatulika,” monga Ufumu wa Mulungu mmene Yesu Kristu, “mwana wa Davide,” akutumikira monga Mfumu ndi Wansembe pa mpando wachifumu. Ili linalinso tanthauzo la uthenga wolengezedwa ndi angelo asanabadwe ndi panthaŵi ya kubadwa kwake mu Betelehemu wa Yudeya, mzinda wa Davide.​—Luka 1:32, 33; 2:10-14; 3:31.

Kuti akwaniritse uminisitala wake wa kuchitira umboni chowonadi Yesu anafunikira kuchita zambiri kuposa kokha kulankhula, kulalikira, ndi kuphunzitsa. Kuphatikiza pa kusiya ulemerero wake wa kumwamba kudzabadwa monga munthu, anafunikira kukwaniritsa zinthu zonse zoloseledwera iye, kuphatikizapo mthunzi, kapena zitsanzo, zolembedwa mpangano la Chilamulo. (Akol. 2:16, 17; Aheb. 10:1) Kuti achilikize chowonadi cha mawu ndi malonjezo aulosi za Atate wake, Yesu anafunikira kukhala ndi moyo m’njira yopangitsa chowonadi chimenecho kukhala chenicheni, akumachikwaniritsa mwa zimene ananena ndi kuchita, mmene anakhalira moyo, ndi mmene anafera. Chotero, anafunikira kukhala chowonadi, m’chenicheni kukhala wodzala ndi chowonadi, monga mmene iyemwini ananenera kuti anali.​—Yohane 14:6.

Chifukwa cha chimenecho mtumwi Yohane anakhoza kulemba kuti Yesu anali “wodzala ndi chisomo ndi chowonadi” ndikuti, ngakhale kuti “Chilamulo chinapatsidwa Mose; chisomo ndi chowonadi zinadza mwa Yesu Kristu.” (Yohane 1:14, 17) Mwa kubadwa kwake kwaumunthu, kudzipereka kwake kwa Mulungu mwa ubatizo wa m’madzi, utumiki wake wapoyera wochilikiza Ufumu wa Mulungu kwa zaka zitatu ndi theka, kufa kwake wokhulupirika kwa Mulungu, kuukitsidwira kwake kumwamba​—mwa zochitika zofunika zonsezi​—chowonadi cha Mulungu chinafika, kapena “chinakhalako,” ndiko kuti, chinapangidwa. (Yerekezerani ndi Yoh. 1:18; Akol. 2:17.) Chotero ntchito yodzisankhira yonse ya Yesu inali ‘yochitira umboni chowonadi,’ zinthu zimene Mulungu analumbira. Motero Yesu sanali Mesiya wophiphiritsira kapena Kristu. Iye anali wolonjezedwa weniweniyo. Iye sanali Mfumu ndi Wansembe wophiphiritsira. Iye, mwamaumboni ndi zenizeni, anali wachowonadi chophiphiritsidwa.​—Aroma 15:8-12; yerekezerani ndi Salmo 18:49; 117:1; Deut. 32:43; Yesaya 11:10.

Chowonadi chimenechi chinali chowonadi chimene ‘chikanamasula anthu’ ngati akadadzisonyeza kukhala “mwa chowonadi” mwa kuvomereza thayo la Yesu m’chifuniro cha Mulungu. (Yoh. 8:32-36; 18:37) Kunyalanyaza chifuniro cha Mulungu chonena za Mwana wake, kuika ziyembekezo pa maziko ena aliwonse, kupanga zosankha za moyo wa munthuwe pa maziko ena aliwonse kukakhala kukhulupirira bodza, kunyengedwa, kutsatira utsogoleri wa atate wabodza, Mdani wa Mulungu. (Mat. 7:24-27; Yoh. 8:42-47) Kukatanthauza ‘kufera m’machimo a munthuwe.’ (Yoh. 8:23, 24) Chifukwa cha chimenechi Yesu sanafooke kulengeza malo ake m’chifuno cha Mulungu.

Zowonadi, iye analangiza ophunzira ake, mowagogomezeradi, kuti asabukitse Umesiya wake kwa anthu (Mat. 16:20; Marko 8:29, 30) ndipotu sikaŵirikaŵiri pamene analankhula za iyemwini mwachindunji kukhala Kristu kusiyapo nthaŵi imene anali okha. (Marko 9:33, 38, 41; Luka 9:20, 21; Yoh. 17:3) Koma molimba mtima ndi mokhazikika anasonyeza umboni wopezeka m’maulosi ndi m’tnchito zake umene unatsimikizira kuti anali Kristu. (Mat. 22:41-46; Yohane 5:31-39, 45-47; 7:25-31) Panthaŵi imene analankhula kwa mkazi wa ku Samariya pa chitsime, Yesu, “atalema ndi ulendo,” anadzidziŵikitsa kwa iye, mwinamwake ncholinga chodzutsa chidwi pa nzika za mumzindawo, ndi kuwaturutsa mumzindawo kudza kwa iye ndicho chomwedi chinatulukapo. (Yoh. 4:6, 25-30) Kudzinenera kokha kukhala Mesiya sikukanatanthauza kanthu kukadapanda kukhala ndi umboni, ndipo pomalizira pake, chikhulupiriro chinafunikira kwa openyererawo ndi omvetsera angati adati avomereze chotulukapo ku chimene umboniwo unasonyako mosaphonya.​—Luka 22:66-71; Yohane 4:39-42; 10:24-27; 12:34-36.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena