‘Uphungu wa M’bukhulo Unagwira Ntchito’
Ndizimene wachichepere wa ku Maryland, U.S.A., akulemba ponena za bukhu la Questions Young People Ask—Answers That Work. “Ndinaŵerenga bukhu lonselo m’masiku aŵiri,” iye akutero, “ndipo sindinakhoze kuleka kuuza anthu ponena za ilo.
“Ndinapeza kuti mutu 6, ‘Why Are My Brother and Sister So Hard to Get Along With?’ (Nchifukwa Ninji Mbale ndi Mlongo Wanga Ali Ovuta Kuchita Nawo?), unandithandiza chifukwa chakuti nthaŵi zina ndimadzimva wansanje kwa mkulu wanga. Koma ndinazindikira mwamsanga mwakuŵerenga kuti sindiyenera kuchita nsanje chifukwa chakuti iye anali ndi kuyenera kwina kumene ine ndinalibe. Pamene kutsutsana kunkati kuyambe, ndinagwiritsira ntchito uphungu wa m’bukhulo. Unagwira ntchito! Tsopano unansi wolimba ukukula pakati pa ine ndi mkulu wanga.”
Kukulira m’nthaŵi zino zamavuto sikosavuta. Achichepere amayang’anizana ndi mikhalidwe yatsopano yambiri ndipo ayenera kupanga zosankha zolimba. Kodi ndiyenera kumwa? Kulandira mankhwala ogodomalitsa? Kodi ndi kachitidwe kati kamene kali koyenera ndi wachiŵalo chosiyana? Achichepere afunikira mayankho ogwira ntchito. Tikulingalira kuti inu ndi ana anu mudzapindula mokulira kuchokera m’bukhuli la zithunzi zokopa, lamasamba 320. Landirani kope mwakudzaza ndikutumiza kapepalaka. K45.00 yokha.
Iyi ndi mbali ina ya ntchito yophunzitsa anthu Baibulo yomwe ikuchitika padziko lonse. Ndalama zoyendetsera ntchitoyi ndi zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu lachikuto cholimba, lamasamba 320 Questions Young People Ask—Answers That Work. Ndatsekeramo K45.00 (Zambia).