“Njira Yabwino Koposadi Yophunzitsira”
Zimenezo ndizo zimene munthu wa ku Springfield, Oregon, U.S.A., ananena ponena za matepi a kaseti a bukhu la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuluyo. (Chingelezi) “Iyi ndi njira yabwino koposadi yophunzitsira aliyense,” akulemba motero. “Uphungu wabwino kwa makolo ndi kwa achichepere umaperekedwadi bwino koposa! Sindingaganize za zirizonse koma ‘zabwino’ zokhazokha zofotokozera njira imene bukhuli laŵerengedwera, mmene nkhanizo zasimbidwira! Tikuthokozani kuchokera pansi pa mitima yathu! Chonde titumizireni makope ena aŵiri owonjezereka. Chonde landirani cheke chotsekeredwa cha matepiwo.”
Alabamu iri ndi matepi a kaseti anayi ndi bukhu la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuluyo. (Chingelezi) Nthaŵi yoseŵera njoposa pang’ono maora asanu. Bukhuli lakonzedwera kuŵerenga ndi achichepere, koma banja lonse lingapindule mwakumvetsera matepiwo pamodzi. Kapena ana angaseŵere matepiwo ndi anzawo.
Imeneyi ndimbali yantchito ya maphunziro a Baibulo kuzungulira dziko lonse imene imachirikizidwa ndi zopereka zodzifunira.
Ndingakonde kulandira alabamu yokongola yofiirira yokhala ndi matepi a kaseti anayi a Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuluyo. (Chingelezi) (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower ya kwanuko kaamba ka chidziŵitso.)