Chitonthozo m’Nthaŵi ya Kusoŵa
Kalata yotsatirayi inalandiridwa kuchokera kwa mwamuna wina mu Baltimore, Maryland, U.S.A.: “Chonde tumizani bukhu lazithunzi lachikuto cholimba lamasamba 192 lakuti Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo? Ndikufuna makope aŵiri, limodzi kaamba ka bwenzi langa. Ndinawona chogawirachi pa kapepala kakang’ono kotchedwa Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Akufa Okondedwa? komwe ndinakalandira pakhomo panga. Ndinaferedwa wokondedwa wanga posachedwapa amene anali wapamtima kwa ine kwa zaka 35, ndipo ndinapeza mawu a pakapepalako kukhala okondweretsa ndi otonthoza kwambiri kwakuti sindinafune kukawononga mwa kudula mbali yolembapo dzina ndi keyala. Zikomo pa kudzipereka kwanu. Kuyambira tsopano kunka mtsogolo ndidzachipanga kukhala chizoloŵezi kuŵerenga mabuku onse amene mumasindikiza.”
Mwachimwemwe, palidi chiyembekezo kwa akufa okondedwa. Landirani umboni wopumitsa mtima m’bukhu lakuti Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo? limodzi ndi katrakiti kakuti Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Akufa Okondedwa? Tangodzazani ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba, lamasamba 192 lakuti Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo? ndi katrakiti kakuti Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Akufa Okondedwa?