Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 8/15 tsamba 32
  • Kodi Ndingalake Motani Chitsenderezo cha Anzanga?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingalake Motani Chitsenderezo cha Anzanga?
  • Nsanja ya Olonda​—1990
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 8/15 tsamba 32

Kodi Ndingalake Motani Chitsenderezo cha Anzanga?

Kalata yochokera kwa ofisala wapolisi ku Chicago ikusonyeza kufunika kwa kudziŵa yankho. Iye akulemba motere:

“Pa January 15, 1990, ndinkazenga mlandu kaidi wa zaka zakubadwda 18 yemwe anabwezedwa ku Chicago kuchokera ku Mississippi pa mlandu yense wa kuthawa. Mbali ya kuzenga mlanduyo inali kutenga katundu wa kaidiyo. Pakati pa zinthu zake panali bukhu la Young People Ask.

“‘Kodi unaliŵerenga bukhuli?’ ndinafunsa motero.

“‘Inde,’ iye anayankha motero, ‘pamene ndinkabisala ku Mississippi, ndinagwira ntchito pa pulazi, ndipo Mboni za Yehova ziŵiri zinandipatsa bukhuli.’ Pamenepo iye anayamba kulira, kusisima mosalamulirika. Pakati pa kusisimako, iye anati: ‘Ndaŵerenga bukhuli nthaŵi zambiri, ndipo mutu umene ndimapitiriza kuuŵerenga mobwerezabwereza ndi wakuti “How Can I Cope With Peer Pressure?”’ Iye anawonjezera kuti: ‘Ndikanakhala kuti ndinali ndi chidziŵitso chimenechi zaka zitatu kapena zinayi zapitazo, sindikanakhala pano lero.’

“Kaidiyo anachotsedwapo, ndipo ndinaŵerenga lipoti lapolisilo ndi zimene iye anauza apolisi. Mu ilo iye anati: ‘Mtsogoleri wa gulu langa anandiuza kutsikira ku khwalala ndi kupha chiŵalo cha gulu lolimbana nalo yemwe ankagulitsa cocaine m’gawo lathu. Ndinachita zimene ndinauzidwa. Ndinawopa kuti ziŵalo zina za gululo zikaganiza kuti ndinali wamantha. Ndinafuna kulandiridwa.’”

Mwinamwake nanunso munadzifunsapo mafunso onga ngati awa: Kodi ndingalake motani chitsenderezo cha anzanga? Kodi ndiyenera kuleka sukulu? Kodi ndimotani mmene ndinganenere kuti toto ku kugonana kwa ukwati usanakhale? Kodi nkuneneranji kuti toto ku mankhwala ogodomalitsa? Izi ndi nkhani zoŵerengeka zokha zofotokozedwa mu Questions Young People Ask​—Answers That Work. Ngati ndinu wosangalatsidwa kulandira kope la bukhu lokhala ndi zithunzi zokongola lamasamba 320 limeneli, chonde dzazani ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.

Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba la Questions Young People Ask​—Answers That Work. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower ya kwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 2.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena