Linagwiritsiridwa Ntchito Kuphunzitsa Kalasi
Buku lakuti Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? linagwiritsiridwa ntchito m’sukulu ya ku California. Wazaka 11 zakubadwa wina akufotokoza mmene zinachitikira. “Ndinali kuyang’ana m’buku la Creation,” akulemba motero,” Ndipo ndinawona kuti panali mitu yoŵerengeka yonena za chilengedwe chakuthambo ndi nyenyezi. Panthaŵiyo mphunzitsi wanga anali kutiphunzitsa za nyenyezi ndi mayendedwe ake.
“Chotero ndinalemba papepala mitu imene angasangalale nayo kuŵerenga, ndipo ndinalipereka kwa iwo limodzi ndi bukulo. Sananene chirichonse kwa miyezi ingapo. Ndiyeno anayamba kutiphunzitsa za nthanthi ya kuphulika kwakukulu. Iwo anati ankaŵerenga buku linalake. Anapita kudesiki lawo ndikutulutsa Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Ndinadabwa kwambiri!
“Anati linali buku labwino koposa onse amene anaŵaŵerenga. Ndiyeno anatsegula bukulo ndikusonyeza kalasi zithunzithunzi. Ndinawona kuti funso lirilonse m’bukulo linayankhidwa ndi kugogomezeredwa. Pamene anali kutiphunzitsa, ankatsegula bukulo, kuŵerenga ndime, ndiyeno kuifotokoza. Pamene nthaŵi ya mayeso inafika, mafunso anachokera m’bukulo mwachindunji. Chotero kunali kosavuta kwa ine kukonzekerera mayesowo. . . . Ndinapeza A.”
Tilingalira kuti nanunso mungapindule ndi bukuli. Ngati mungakonde kulandira kope, chonde dzazani ndikutumiza kapepala kali pansipa.
Ndingakonde kulandira buku lachikuto cholimba lamasamba 256 lakuti Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakumaloko kaamba ka chidziŵitso.)
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
NASA photo