Dziko Latsopano Liri Pafupi!
PALI zinthu zambiri zothetsera zoipa za dziko. Mwachisawawa, izo zimaitanira kudera nkhaŵa ndi kugwirizana, limodzinso ndi kuyesayesa kogwirizana kwa mitundu yonse padziko. Pali lingaliro lakuti pamene mikhalidwe ikuipiraipira, kufunika kwa kusungirira kogwirizana kudzakakamiza mitundu kusanthulanso zoyambirira zawo ndi kugwirira ntchito pamodzi kupanga dziko latsopano lochilikizika. Kukuwonedweratu kuti ndalama zankhondo zidzachepetsedwa kwakukulu m’chiyanjo chogwiritsira ntchito chuma ku zothetsera mavuto a malo otizinga ndikuti, monga momwe kwasonyezedwera mu State of the World 1990, “m’malo mosungirira malo awoawo ochinjirizira, maboma angadalire pa gulu losungitsa mtendere la U.N., lofutukulidwa ndi lopatsidwa nyonga, limene likakhala ndi mphamvu ndi ulamuliro wakuchinjiriza dziko lirilonse lomwe liri chiŵalo molimbana ndi woukira.”
Koma makonzedwe oterowo akulephera kotheratu kubweretsa mikhalidwe imene ikulakalakidwa imene inandandalitsidwa pamasamba athu otsegulira. Zoyesayesa za anthu wamba sizingathetse konse kuchimwa kwa anthu ndi umbombo; iwo samachotsa kunyada ndi kukangana kwa mafuko; iwo samalimbitsa chikondi chopanda mpeni kumphasa pakati pa anthu; ndiponso sangathe kutsimikizira mapeto a matenda ndi imfa. Upandu sukulankhulidwapo mokhutiritsa, ndipo palibenso kutchulidwa kwa kulaka kupambadzukana maganizo kwa chipembedzo ndi udani. Ndipo kuchotsa masoka achilengedwe sikungatchulidwe nkutchulidwa komwe. Utundu, wokhala ndi mphamvu yoyambitsa mavuto, waloledwa kukhalirira. Pamenepo, mopanda chimwemwe, tiyenera kutsimikizira kuti anthu alephera kutulutsa yankho lokhoza kugwira ntchito.
Komabe, yankho liripo! Ndithudi, zinthu zonsezi zomwe zikulakalakidwa ndi anthu zinalonjezedwa, ndipo lonjezolo limachokera kwa Mulungu “wosanamayo.” (Tito 1:2) Iye amadziŵadi zimene ziyenera kuchitidwa, ndipo ali ndi nzeru, mphamvu, ndi luso lokwaniritsira zimene akufuna.—Chibvumbulutso 7:12; 19:1.
Mulungu akulonjeza kuti: ‘Katsala kanthaŵi ndipo oipa adzatha psiti; Inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.’—Salmo 37:10, 11.
Kodi ichi chidzakwaniritsidwa motani? Yesaya 11:9 akuyankha motere: ‘Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.’ Inde, anthu onse adzalangizidwa ‘m’kudziŵa Yehova,’ ndipo munthu aliyense wokana kugwirizana ndi zimenezo sadzaloledwa kukhala kuti awononge mtendere wa ena. Dziko lathu lapansi lokongola silidzaipitsidwanso.
‘Penyani ntchito za Yehova. . . . Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi,’ likulonjeza tero Salmo 46:8, 9. (Onaninso Mika 4:3, 4.) Nsonga yofunika yopangitsa mtendere wa dziko lonse umenewu ndiyo kutha kwa kupambadzukana maganizo kwa utundu. Kugwirizana n’kotsimikizirika, chifukwa chakuti padzakhala boma limodzi lokha padziko lonse—lija la Mulungu. Ndipo boma lake ndilo Ufumu “woti sudzaonongeka.” (Danieli 2:44) Kuwonjezerapo, Mfumu yake ndiye Yesu Kristu woukitsidwa, wokhala ndi moyo wosakhoza kufa, amene ulamuliro wake udzakhala wa chiweruzo ndi chilungamo.—Yesaya 9:6, 7; 32:1.
Koma kodi ichi chidzaipitsidwa ndi kupanda ugwiro kobadwa nako kwa munthu ndi kudetsedwa ndi kupweteka kosalekeza, matenda, chisoni ndi imfa? Ayi, popeza kuti izinso zidzakhala zinthu zakale. Chibvumbulutso 21:4 chikutitsimikizira motere: ‘Ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.’ Chimo lacholowa lidzakhululukidwa pamaziko a nsembe yadipo ya Yesu, ndipo anthu adzabwezeredwa ku mkhalidwe wangwiro. (Aroma 6:23; Aefeso 1:7) Ndipo kodi ndani amene angalamulire bwinoko mphamvu zachilengedwe ndi kuziletsa kubweretsa chivulazo pa anthu kuposa Mlengi wawo?—Salmo 148:5-8; Yesaya 30:30.
Zinthu zimene munthu angaziyembekeze ndi kuzilota, nzimene Mulungu adzazichita. Koma liti? Ulosi wa Baibulo ukusonyeza kuti masinthidwewo adzachitika panthaŵi imene mitundu idzakhala ‘yokwiya’ ndipo munthu adzakhala ‘akuwononga dziko.’ (Chibvumbulutso 11:18) Masiku omaliza a dziko lakaleli akazindikiritsidwa ndi “nthawi zowawitsa”—kutulukapo mikhalidwe yoipirapo imene tikuiwona tsopano. (2 Timoteo 3:1-5, 13) Ndipo Yesu ananeneratu kuti mbadwo umene ukawona zinthu zoterozo ukakhala mbadwo umene unawona kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu.—Mateyu 24:3-14, 32-34.
Patulani nthaŵi ya kufufuza m’malonjezo amene alembedwa m’Baibulowa. Popeza kuti, onse aŵiri anthu achidziŵitso ndi Mulungu akugwirizana pamfundo iyi: Ino tsopano ndiyo nthaŵi ya dziko latsopano!