Kufikira Mulungu Kovuta
‘INE ndine njira, ndi chowonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa ine,’ anatero Yesu Kristu. Iye anawonjezera kuti: “Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m’dzina langa.”—Yohane 14:6; 16:23.
Komabe, kwa zaka mazana ambiri, zipembedzo za Chikristu Chadziko, makamaka Tchalitchi cha Roma Katolika, ndi ziphunzitso zake za moto wa helo, purigatoriyo, ndi Utatu, zasokoneza “njirayo.” Yesu anasonyezedwa, osati monga mtetezi wofunitsitsa wa anthu ochimwa, koma monga khanda lokhala m’manja kapena monga woweruza wochititsa mantha, wokhoterera kwambiri kuweruza ndi kulanga anthu ochimwa mmalo mowapulumutsa. Pamenepo, kodi munthu wochimwa angamfikire motani Mulungu?
Bukhu lakuti The Glories of Mary (1750) likulongosola. Poyerekezera Yesu ndi dzuŵa lotentha la chilungamo, papa Innocent III wa m’zaka za zana la 13 analengeza kuti: “Munthu aliyense amene ali mumdima wa tchimo, apenye ku mwezi, achonderere kwa Mariya.” Mariya, amake wa Yesu, anapangidwa kukhala mtetezi wina. Mwinamwake kupyolera m’chisonkhezero chake cha unakubala, chiyanjo chingapezedwe kuchokera kwa Yesu ndi kwa Mulungu. Chotero, m’mawu a Laurence Justinian, mtsogoleri wachipembedzo wa m’zaka za zana la 15, Mariya anakhala “makwerero opitira ku paradaiso, chipata cha kumwamba, nkhoswe yeniyeni pakati pa Mulungu ndi anthu.”
Popatsidwa ulemu wonsewo, m’kupita kwa nthaŵi iye sanawonedwe kokha monga “Namwali Mariya” koma anakhala “Mfumukazi Yoyera, Mayi wa Chifundo,” wolinganizidwa mwaluso monga wosachimwa ndi wokwezedwa kwakuti analinso wopatulikitsa wosatheka kufikiridwa mwachindunji. Kodi mtetezi wina akapezekanso? Bwanji ponena za amayi ake?
Popeza kuti Baibulo silimanena kanthu pankhaniyi, yankho linafunidwa kwinakwake. Bukhu la Apocryphal, Protevangelium of James likusimba nkhani ya Anne (kapena Anna), mkazi wa Yoakimu, amene analibe mwana kwa zaka zambiri za ukwati. Pomalizira pake, mngelo anawonekera kwa iye ndikulengeza kuti akabala mwana. Kukunenedwa kuti m’kupita kwanthaŵi, anakhala amake wa “Namwali Mariya.”
Chotero panabuka dzoma la Anne “Woyera.” Akachisi ndi matchalitchi anamangidwa momulemekeza. Kulambiridwa kwa Anne “Woyera” kunakhala kofala mu Yuropu m’zaka za zana la 14.
“Ha, chipembedzo chinakhala chovuta chotani nanga!” likutero bukhu la The Story of the Reformation. “Anthu ankapemphera kwa Anna yemwe anachonderera kwa Mariya yemwe anachonderera kwa Mwana wake amene anachonderera kwa Mulungu kaamba ka anthu ochimwa. Zinali zosangalatsa, komatu chimenechi chinali chikhulupiriro chamalaulo pachimene miyoyo ya anthu inamangidwapo.” Pamenepo, panopo pali malo ena pamene mawu a Yesu akugwira ntchito moyenerera: ‘Muyesa achabe mawu a Mulungu mwa mwambo wanu.’—Marko 7:13.
[Mawu a Chithunzi patsamba 21]
The Metropolitan Museum of Art, Bequest of Benjamin Altman, 1913. (14.40.633)