Kodi Nchifukwa Ninji Mulungu Walola Kuipa?
SATANA Mdyerekezi, yemwe anachititsa mwamuna ndi mkazi woyamba, Adamu ndi Hava, kupandukira Mulungu, ngwotsutsana ndi muyezo wolungama wa Mulungu ndipo moyenerera akutchedwa “woipayo.” (Mateyu 6:13; 13:19, 38; 1 Yohane 2:13, 14; 5:19) Chipanduko choyambitsidwa ndi Satana chinakaikiritsa kuyenerera ndi kulungama kwa ufumu wa Mulungu, ndiko kuti, kaya ulamuliro wa Mulungu pa zolengedwa zake ukuchitidwa mwachilungamo ndi kaamba ka zikondwerero zawo zabwino koposa. Mfundo yakuti Adamu ndi Hava anapanduka inadzutsanso nkhani iyi: Kodi zolengedwa zina zonse zaluntha zikatsimikizira kukhala zosakhulupirika ndi zosamvera Mulungu pamene chimvero chikawonekera kukhala chosadzetsa mapindu akuthupi? Chinenezo cha Satana kulinga kwa Yobu wokhulupirika chinatanthauza kuti iwo akatero. Satana anati: ‘Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuwombola moyo wake. Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.’—Yobu 2:4, 5.
Panafunikira nthaŵi kuti nkhani zodzutsidwazo zithetsedwe. Chotero, kulola kwa Yehova Mulungu, anthu oipa kupitirizabe kukhalapo ndi moyo, kunatheketsa ena kukhalamo ndi phande m’kutsimikizira chinenezo cha Satana kukhala chonama mwakutumikira Mulungu mokhulupirika pansi pamikhalidwe yovuta ndi yopereka chiyeso. Kulola kuipa kwa Mulungu kwaperekanso mwaŵi wakuti anthu achoke ku njira yoipa ndikudzigonjeretsa mofunitsitsa ku malamulo olungama a Mulungu. (Yesaya 55:7; Ezekieli 33:11) Chotero kuimitsa kwa Mulungu chiwonongeko cha anthu oipa kwanthaŵi yakutiyakuti kukutumikira kupulumutsa amaganizo olungama mwakuwapatsa nthaŵi kutsimikizira chikondi ndi kudzipereka kwawo kwa Yehova.—Aroma 9:17-26.
Kuwonjezerapo, Yehova Mulungu amagwiritsira ntchito mikhalidwe mwanjira yakuti oipa iwo eniwo mosadziŵa atumikire chifuno chake. ngakhale kuti amatsutsa Mulungu, iye angawatsekereze kwautali wofunika kuti atumiki ake asungikebe mu umphumphu wawo, ndipo angapangitse zochita za anthu oterowo kukwaniritsa chilungamo chake. (Aroma 3:3-5, 23-26; 8:35-39; Salmo 76:10) Lingaliro limeneli lalongosoledwa pa Miyambo 16:4 kuti: ‘Zonse Yehova anazipanga ziri ndi zifukwa zawo; ngakhale amphulupulu kuti awone tsiku loipa.’
Nkhani yofotokoza mfundoyi ndiyo ya Farao amene Yehova, kupyolera mwa Mose ndi Aroni, anatumikira monga populumutsira Aisrayeli okhala muukapolo. Mulungu sanapangitse wolamulira Wachiiguptoyu kukhala woipa, koma anamulola kupitirizabe kukhala ndi moyo ndipo anachititsanso mikhalidwe imene inapangitsa Farao kudzisonyeza mwiniyekha kukhala woipa ndiwoyenerera imfa. Chifuno cha Yehova chakuchita chimenechi chavumbulidwa pa Eksodo 9:16 motere: ‘Koma ndithu chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuwonetse mphamvu yanga, ndikuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.’
Miliri Khumi imene inagwa pa Igupto, niifika pachimake mwakuwonongedwa kwa Farao ndi magulu ake ankhondo m’Nyanja Yofiira, inali chisonyezero chochititsa chidwi cha mphamvu ya Yehova. (Eksodo 7:14–12:30; Salmo 78:43-51; 136:15) Zaka zambiri pambuyo pake mitundu yozungulira inkasimbabe za icho, ndipo motero dzina la Mulungu linalengezedwa padziko lonse lapansi. (Yoswa 2:10, 11; 1 Samueli 4:8) Yehova akadamupha Farao mofulumira, chisonyezero chachikulu cha mphamvu ya Mulungu chimenechi kuulemerero Wake ndi kupulumutsidwa kwa anthu Ake sichikanatheka.
Malemba amapereka chitsimikiziro chakuti nthaŵi idzafika pamene kuipa sikudzakhalaponso, popeza kuti onse otsutsa Mlengi adzawonongedwa pamene chifuno cha kulola kwake kuipa chidzakwaniritsidwa.—2 Petro 3:9-13; Chibvumbulutso 18:20-24; 19:11–20:3, 7-10.