“Mankind’s Search for God”
“Bukhuli linandikondweretsa kwenikweni ndikunditenga maganizo kwakuti sindinathe kuliika pansi,” analemba motero woŵerenga wa ku Houston, Texas, U.S.A. Iye anati m’dera lake muli anthu pafupifupi achipembedzo chirichonse chofotokozedwa m’bukhuli, komabe anavomereza kuti: “Sindinamvetsetse zikhulupiriro zawo zazikulu ndimmene ndingawatsogozere iwo ku Baibulo kaamba ka mayankho. Bukhuli lakhala yankho ku mapemphero anga.”
Bukhu la Mankind’s Search for God liri ndi kufufuza kopendedwa mosamalitsa kotheratu, kukambitsirana kwakuya kwa zipembedzo zonga Chihindu, Chibuda, Chitao, Chikonfyushani, Chishinto, Chisilamu, ndi Chiyuda. Woŵerenga wa ku Texas ameneyo anati: “Bukhuli limafotokoza zikhulupiriro za anthu ena mwanjira yolingalirika ndi yaulemu, pamene limawalimbikitsa kupitirizabe kufunafuna kwawo Mulungu wowona, Yehova. Ndipo mawu amabwera mwachindunji kwa iweyo, monga ngati kuti winawake wakhala moyandikana nawe mukumakambitsirana.”
Tikhulupirira kuti bukhu lamasamba 384 limeneli la Mankind’s Search for God lidzayankha ambiri a mafunso anu. Ngati mungakonde kulandira kope, tangodzazani ndikutumiza kapepalaka ku keyala yoperekedwa pansipa.
Ndingakonde kulandira bukhu lokhala ndi zithunzithunzi lamasamba 384 la Mankind’s Search for God. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakumaloko kaamba ka chidziŵitso. Onani patsamba 2.)
[Zithunzi patsamba 32]
Chikristu Chadziko
Chisilamu
Chihindu
Chikonfyushani—Chitao—Chibuda
Chibuda
Chishinto
Chiyuda
Zipembedzo Zamwambo