Kodi Mungakonde Kuchezeredwa?
Chaka chatha mkazi wina wa ku Corpus Christi, Texas, U.S.A., analembera kalata Watchtower Society ku Brooklyn, New York, kuti: “Dzina langa ndine Emily, ndipo ndakhala ndikuphunzira mabuku amene ena a Mboni za Yehova anandipatsa milungu ingapo yapita. Pambuyo poŵerenga magaziniwo ndi kuwayerekezera ndi Baibulo la banja langa, ndinapeza kuti Tchalitchi cha Roma Katolika sichinkaphunzitsa zimene zinali m’Baibulo Lopatulika. Iwo sanatchule konse dzina la Mulungu kapena kudza kwa Ufumu wa Mulungu, zimene ndapeza kukhala nkhani zazikulu m’Baibulo langa. Ndaleka kupita ku tchalitchi cha banja langa ndipo ndayamba kuphunzira Baibulo, ndiyamikira kwambiri mabuku anu a chowonadi.
“Ndingakonde kuyamba kuyanjana ndi mpingo wa kuno wa Mboni za Yehova. Chonde atumizireni uthenga kuti akabwere kunyumba kwanga kuti tikakambitsirane.”
Mmodzi wa Mboni za Yehova angakonde kukuchezerani ndi kukuthandizani kuwonjezera chidziŵitso chanu chonena za Mulungu, Ufumu wake, ndi zifuno zake, monga momwe zalembedwera m’Baibulo. Kuti mupindule ndi utumiki umenewu, tangolembani mawu ofunidwa pansipa ndi kutumiza ku keyala iri pakapepalaka.
Ndingakonde kudziŵa zowonjezereka ponena za Baibulo. Chonde linganizani kuti wina adzandichezere.