“Linandigalamutsa”
Izi ndizimene mkazi wina ku Washington State, U.S.A., ananena za bukhu la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Anafotokoza kuti:
“Kwa zaka zinayi m’modzi wa Mboni za Yehova anabwera pakhomo langa nthaŵi zonse ndi kusiya magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Iye anandilimbikitsa kuphunzira. Pomalizira pake ananditheketsa kuŵerenga bukhu la Creation, ndipo ndinatero. Anandilimbikitsa kupemphera, ndipo ndinatero. Bukhu limeneli linachotsa zikaikiro zonse, ndipo pemphero linadzetsa chithandizo kuchokera kwa Yehova. . . .
“Tsopano ndimadziŵa kuti Mulungu alikodi. Ndimadziŵa dzina lake, Yehova. Ndidziŵa kuti amamva mapemphero. Ndidziŵa chifukwa chake zinthu zakhalira monga momwe ziriri. Ndiri pa mtendere, ndipo mtendere wanga umakula mlungu uliwonse pamene ndiphunzira zowonjezereka.”
Bukhu lokongola limeneli, limodzi ndi malongosoledwe ake olondola a chilengedwe ndi tsatanetsatane wonse wocholoŵana amene amapangitsa moyo kukhala wothekera padziko lapansi zidzakuchititsani chidwi. Mungalandire kope mwakudzaza ndi kutumiza katikiti kotsatiraka.
Ndingakonde kulandira bukhu la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? (Kunja kwa Zambia, lemberani thambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani patsamba 2.)
[Chithunzi patsamba 32]
Akatswiri achisinthiko amati: “Sikumavutitsa maganizo kwenikweni kuwona nthenga monga mamba okulitsidwa [a chamoyo chokwawa].” Zenizeni zimasonyeza zosiyana
Shaft
Barbs
Barbules
Barbiceles