Kufunafuna Mtendere Wamaganizo
Zimenezo ndi zomwe mkazi wina wa ku Salt Lake City, Utah, U.S.A., ananena kuti wakhala akuzifunafuna m’chipembedzo kwa zaka zambiri. Iye akulemba kuti: “Kufikira miyezi isanu ndi itatu yapitayo, ndinalingalira kuti sindikakhala konse ndi mtendere wamaganizo. Ndiyeno Mboni zinafika pakhomo panga mu February. Ndakhala ndikuphunzira kwa miyezi isanu ndi itatu, ndipo ndazindikira kuti ndinu nokha amene mukukonzekeretsa anthu kaamba ka Ufumu wa Mulungu.”
Mkazi ameneyu anawonjezera kuti: “Tsiku lina bwenzi langa lomwe ndi Mboni linandipatsa bukhu lotchedwa Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? Sindinasangalalepo ndi bukhu mokulira monga momwe ndinachitira ndi ili. Ndithudi, ilo liri limodzi la mabuku abwino koposa a Watch Tower Society.”
Ngati mukufuna kulandira kope la bukhu labwino limeneli, chonde dzazani ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba lamasamba 192 la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi ya Watch Tower yakwanuko kaamba ka chidziŵitso. Onani patsamba 2.)
[Chithunzi patsamba 32]
Maulosi a Danieli onena za maulamuliro adziko anakwaniritsidwa molondola kwakuti osuliza amakono amaganiza kuti analembedwa pambuyo pa kukwaniritsidwa kwawo