‘Bukhulo Lingosoŵasoŵa’
Izi nzimene mphunzitsi wamkazi wa pasukulu yasekondale kum’mwera kwa California, U.S.A., akunena ponena za bukhu la Questions Young People Ask—Answers That Work. Sukuluyo inayambitsa nyengo ya kuŵerenga kwa tsiku ndi tsiku mu imene ophunzira akhoza kuŵerenga chirichonse chimene anakonda. Iye anapereka mabuku, kuphatikizapo bukhu la Young People Ask, kaamba ka ophunzira omwe sanabweretse choŵerenga.
“Bukhulo lakhala lokondedwa koposa m’kalasi,” iye akufotokoza tero. “Nthaŵi zina limasoŵa kwa maola angapo, kapena ngakhale kwa tsiku limodzi kapena aŵiri, ndiyeno limabweranso. Ophunzira amafunsa anzawo, ‘Kodi unaliŵerenga iri?’ kapena kupereka ndemanga kuti, ‘Bukhu lija nlabwino kwabasi.’ Pambuyo pofotokozera mabwenzi awo, iwo amabwerera kukaŵerenga zowonjezereka.
“Masamba amapindidwa, ndipo bukhulo likusonyeza zizindikiro za kung’ambika. Mutu wong’ambika kwambiri ndi wa 23, ‘What About Sex Before Marriage?’ Ophunzira amakonda zithunzithunzi, ndipo amazitchula ndi mitu yake. Ndinawona wophunzira wina akuŵerenga mutu wakuti ‘Why Did Dad and Mom Split Up?’
“Pambuyo panthaŵi yochepa bukhu loyamba linasoŵa, choncho ndinaikapo lina. Ndiyeno loyambalo linabwerera, chotero pali aŵiri tsopano. Papita miyezi itatu kapena inayi chiyambire pamene ndinaikirapo bukhu loyambalo, ndipo iwo adakali kuŵerengedwa.”
Nayi mitu ina pakati pa yokwanira 39 m’bukhumo “How Can I Make Real Friends?” “How Important Are Looks?” ndi “How Do I Know If It’s Real Love?” Ngati mungakonde kulandira kope la bukhu la zithunzithunzi zokopa limeneli, chonde dzazani ndi kutumiza kapepalaka.
Ndingakonde kulandira bukhu lachikuto cholimba lamasamba 320 la Questions Young People Ask—Answers That Work. (Kunja kwa Zambia, lemberani nthambi yakwanuko ya Watch Tower kaamba ka chidziŵitso. Onani tsamba 2.)