Kodi Nchiyani Chidzachitikira Malo Opatulika a Chikristu Chadziko?
OFALITSA bukhu la Holy Places of Christendom, lolembedwa ndi katswiri wofufuza zam’mabwinja Stewart Perowne, anafunsa kuti: “Kodi ndani, mosasamala kanthu za mwambo Wachikristu umene angachokereko, amene angaime pa Kalivali m’Tchalitchi cha Chiukiriro [kapena, Tchalitchi cha Manda Opatulika] ku Yerusalemu popanda kuchita mantha: popeza kuti malo olemekezeka ameneŵa ndipo olimbaniridwadi kwa zaka mazana ambiri, ndiwo malikulu a Chikristu Chadziko.”
Palibe amene wakhala wokhoza kupereka umboni wotsimikizira wakuti tchalitchi chimenechi chinamangidwa pa Kalivali, malo amene Yesu Kristu anaferapo. Ndiiko komwe, Constantine wolamulira wa Roma asanasankhe kumangapo tchalitchi pamenepo, panali kale kachisi wachikunja. Ndiponso, Yesu anati: ‘Mulungu ndiye Mzimu; ndipo omlambira ayenera kumlambira mumzimu ndi m’chowonadi.’ (Yohane 4:24) Olambira oterowo samalemekeza malo “opatulika” akuthupi.
Panthaŵi ina, Yerusalemu anali malo a kachisi wa Mulungu motero anali malikulu akulambira koyera. Komabe, chifukwa cha kusakhulupirika kwa nzika za mzindawo, Yehova Mulungu anaukana, monga momwe Yesu ananenera kuti akatero. (Mateyu 23:37, 38) Yesu ananeneratunso za kugwa kwa malikulu achipembedzo amenewo, amene ambiri anapitiriza kuwawona kukhala malo opatulika. Mawu ake anakwaniritsidwa pamene Aroma anawononga Yerusalemu ndi kachisi wake mu 70 C.E.—Mateyu 24:15, 21.
Posachedwapa, ulosi wa Yesu udzakhala ndi kukwaniritsidwa kwakukulu pa ufumu wonse wachipembedzo wa Chikristu Chadziko, umene chimanena kuti ndimalo opatulika. Chikristu Chadziko ndi malo ake opatulika tsopano chiri pafupi kuwonongedwa ndi gulu losakhala lachipembedzo lotchedwa ‘chonyansa chopululutsa.’ (Danieli 11:31) Mboni za Yehova zidzakhala zokondwa kukupatsani chidziŵitso chonena za mmene chochitika chochititsa mantha chimenechi chidzachitikira.
[Chithunzi patsamba 32]
Malo olambirira mkati mwa Tchalitchi cha Manda Opatulika
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.