Siiri Chabe Mizati Yochititsa Chidwi
Alendo amachita chidwi ndi mizati ya ku nyanja ya Mediterranean ku Kaisareya, doko lamakedzana kugombe la Israyeli. Herode Wamkulu anamanga doko limeneli natcha mzindawo dzinalo kulemekeza Kaisara Augusto.
Akatswiri ofukula zam’mabwinja anapeza mbali yaikulu ya mzindawo, kuphatikizapo bwalo lalikulu lamaseŵera. Ndiponso aloŵa pamadzi kukapeza chidziŵitso cha mmene dokolo linamangidwira pagombe lamchenga.
The New York Times (January 8, 1991) inasimba za kutumbidwa kwa mizati m’mabwinja a nyumba yachifumu imene kale inaloŵako m’nyanja. Imeneyi njapadera pakuti zozokotedwapo zimatchula abwanamkubwa a Roma amene anali osadziŵika konse. “Kapitawo” wa zombo amatchulidwanso, chimene “chili chozokotedwa choyamba chopezedwa chomwe chimanena za dokolo.”
Ophunzira Baibulo amadziŵa kuti mtumwi Paulo anakocheza padoko limeneli pamapeto pa maulendo aŵiri aumishonale. Anakhala panopa ndi mlaliki Filipo, ndipo zokumana nazo zake ziyenera kuti zinawalimbikitsa kwambiri ophunzira. (Machitidwe 18:21, 22; 21:7, 8, 16) Tikhoza kuŵerenga zokumana nazo zosangalatsa zambiri zimenezi m’bukhu la Baibulo la Machitidwe a Atumwi.
Choncho mizati imeneyi kugombe la nyanja siiri chabe zotsala za m’mbiri zopanda pake. Imaŵakumbutsa Akristu amakono za abale awo oyambirira, amene anafalitsa mbiri yabwino mwachangu kumadoko ndi ‘malekezero ake a dziko.’—Machitidwe 1:8.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Garo Nalbandian