Mukuitanidwa Mwachimwemwe
Imfa ya munthuyo Yesu Kristu zoposa zaka 1,900 zapitazo inali chochitika chofunika kwambiri m’mbiri. Inatitsegulira tonsefe chiyembekezo chakulandira moyo wosatha pansi pamikhalidwe Yaparadaiso. Pachochitika chosacholoŵana, Yesu anagwiritsira ntchito vinyo ndi mkate wopanda chotupitsa monga ziphiphiritso za nsembe yake yaumunthu yachikondi. Ndiyeno anauza ophunzira ake kuti: ‘Chitani ichi chikumbukiro changa.’ (Luka 22:19) Kodi mudzakumbukira?
Mboni za Yehova zikukuitanani mosangalala kutsagana nazo kusunga phwando Lachikumbutso limeneli. Lidzachitidwa dzuŵa litaloŵa padeti lolingana ndi Nisani 14 pa kalenda yamwezi ya Baibulo. Mungapezekepo pa Nyumba Yaufumu yapafupi ndi kwanuko. Funsani Mboni za Yehova zakumaloko nthaŵi yeniyeni ndi malo. Deti la phwandolo mu 1992 lidzakhala Lachisanu, April 17.