Tsiku Loyenera Kulikumbukira
Madzulowo Yesu asanaphedwe, anagaŵana mkate wopanda chotupitsa ndi vinyo ndi atumwi ake nati: ‘Chitani ichi chikumbukiro changa.’—Luka 22:19. Chaka chino, phwando lapachakalo limene analangiza lidzakhala pa April 17, dzuŵa litaloŵa.
Choncho, Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse zidzasonkhana madzulo apadera ameneŵa kuchita Chikumbutso chimenechi mwanjira imene Yesu analangiza. Mukulandiridwa ndi manja aŵiri kudzasonkhana nafe. Chonde funsani Mboni za Yehova zakwanuko ponena za nthaŵi yeniyeni ndi malo osonkhanirako.