Moto Usonkhezera Programu Yakumanga
“MOTO! Moto! Holo Yosonkhanira ya Mboni za Yehova ikupsa!” Mfuu yodzidzimutsa imeneyo inamveka pa Lachisanu masana mu October 1989 ku Heerenveen, tauni yakudera lakumpoto kwa Netherlands.
Mboni za Yehova zinagwiritsira ntchito Holo Yosonkhanira yokongola imeneyo kwa zaka 11. Pafupifupi pakutha kwa mlungu uliwonse, mazanamazana ankasonkhana kumeneko kaamba ka msonkhano wadera wamasiku aŵiri kapena tsiku la msonkhano wapadera. Inali malo abwino olandirira malangizo a Baibulo.
Ngozi inawoneka pamene ntchito yokonza tsindwi la holoyo inali mkati. M’mphindi zochepa zokha, ngozi imeneyo inasanduliza holoyo kukhala bwinja la moto wotukutira. Komabe, mwamwaŵi, palibe anavulala.
Pokhala zachisoni ndi kutaikiridwako koma zosalefulidwa, Mbonizo zinapanga makonzedwe akumanga holo yatsopano pamalo ena. Zinapeza malo oyenera ku Swifterbant, kudera la Flevoland. Malo amenewo ndichidikha chachikulu kumtunda chomwe kale chinali Zuider Zee, cha mamita 5 kuchoka pamwamba pa nyanja.
Pofika January 1991 chilengezo chinaperekedwa chakuyamba kumanga Holo Yosonkhanira yatsopano. Ikamangidwa pakati pa May ndi September 1991. Mboni mazana ambiri zinadzipereka modzifunira kukagwira ntchito kumalowo, ndipo anyamata ena anawona chimangocho kukhala njira yoyambira kutumikira Yehova Mulungu nthaŵi zonse. Antchito ambirimbiri anadza kuchokera ku Belgium ndi Mangalande.
Nyumba yolinganizidwa bwino inamangidwa. Malo okhala omvetsera ndi kafeteriya nzolumikizana ndi njira yofoleredwa ndi tsindwi lamagalasi. M’holo yaikulu mumakhala anthu 1,008, ndipo anthu ena okwanira 230 amawonerera programuyo pawailesi yakanema m’holo yapafupi.
Lerolino, anthu zikwi zambiri amati: ‘Tiyeni tikwere kumka ku phiri la Yehova, ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake.’ (Yesaya 2:2, 3) Holo Yosonkhanira yatsopano imeneyi ili kokha imodzi mwa malo ambiri kumene malangizo auzimu otero amaperekedwa. Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova yakwanuko ndiyo malo ena. Kumeneko mudzalandiridwa bwino kwambiri.