Angaphunzire kwa Njuchi
“M’zaka zaposachedwapa, ainjiniya ndi amisiri akhala akuzindikira mowonjezereka kanthu kena kamene mwachiwonekere njuchi zakadziŵa nthaŵi zonse: kuti kuumba kanthu kopyapyala kwambiri mumpangidwe wa mbali zisanu ndi imodzi wonga kachipinda ka chisa cha njuchi kumalimbitsa kanthuko koposa mmene kangakhalire ngati kaumbidwa mumpangidwe wina wosiyana.”—The New York Times, October 6, 1991.
NKOSADABWITSA kuti anthu angapindule mwakupenda tizilombo mosamalitsa. Mwamuna wamakedzana wokhulupirika, Yobu, nthaŵi ina anati: “Tafunsira tsono kwa nyamazo, zidzakulangiza, ndi mbalame za m’mlengalenga, zidzakuuza; . . . Ndaniyo sadziŵa nazo izi zonse; kuti dzanja la Yehova lichita ichi?” (Yobu 12:7-9) Inde, nzeru ya Mlengi imawonekera m’zinthu zofala monga kaumbidwe kambali zisanu ndi imodzi ka tizipinda tomwe mumawona m’chisa cha njuchi.
Ngakhale kuti makoma aphula a zisa zimenezi ali chabe ochindikala ndi pafupifupi limodzi la magawo atatu a milimita, ngolimba zedi. Kunena zowona, akhoza kuchirikiza kulemera kwawo kwenikweniko kutaŵirikizidwa kwanthaŵi 30.
Kulimba koteroko kungagwiritsidwe ntchito mwanjira zothandiza, zonga ngati kutetezera zipangizo zimene zimagunda kuzinthu. Kumatetezeranso ngakhale zida zankhondo zoponyedwa kuchokera m’ndege ndi mapalatchuti. Ponena za zimenezo, The New York Times inati: “Zipangizo zolema kwambiri mofanana ndi magalimoto ankhondo a jeep zimamangidwa pazokhazikapo zimene kunsi kwake kumakhala zinthu zampangidwe wa zisa za njuchi zimene zimachepetsa mphamvu yakugunda pansi potera.”
Zinthu zopangidwa ndi anthu zampangidwe umenewo zingapangidwe mogwiritsira ntchito zopangira zambiri zosiyanasiyana. Chofala kwambiri ndicho pepala. Mapepala opangidwa ndi nylon ndi maliroliro amagwiritsiridwa ntchito kupangira zinthu zonga zisazo zoika m’makoma a zipinda za ndege zina zazikulu zokweramo anthu. Kulimbako kumachititsa kupepuka. Chifukwa? Chifukwa chakuti mipata yambiri pakati pa makomawo njodzala mpweya, siolemera kwambiri. Ndiponso mpweya umachinjirizanso kutentha.
Kanjuchi “sikamadziŵa” zonsezo, pakuti kalibe digiri iriyonse m’maphunziro azauinjiniya. Komabe, masiku onse kamachita ntchito yake mothandizidwa ndi nzeru yachibadwa yoperekedwa ndi Mlengi, Yehova.