Anafika Mosasamala Kanthu za Mavuto ndi Upandu
DETILO linali January 2, 1992. Malo ake—Maxixe, Chigawo cha Inhambane. Mapokoso ausiku a mu Afirika mu Mozambique anadodometsedwa mwadzidzidzi pamene wailesi inatsegulidwa. “Mboni za Yehova zikuchita Msonkhano wawo Wachigawo wakuti ‘Okonda Ufulu’ m’chigawo chathu chino,” woulutsa pawailesiyo analengeza motero. “Chifuno chawo ndicho cha kulangiza anthu za mmene ufulu weniweni ungapezedwere m’dziko lamakonoli. Anthu onse akuitanidwa kuti afikepo.”
Kumbali imeneyo ya Afirika kutalitaliko, mbiri yosaiŵalika inalinkupangidwa! Kwanthaŵi yoyamba, msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova unalinkuchitika, ndipo anthu 1,024 anali kumeneko kukasangalala nawo. Zaka zoŵerengeka zapitazo, chochitika choterocho sichikanachitika poyera m’Mozambique, popeza kuti ntchito ya Mboni za Yehova panthaŵiyo inali yoletsedwa. Kodi mukakonda kumva za kudzimana kolimba mtima kumene kunapangidwa kukakhala nawo pamsonkhano wachigawowu?
Chigawo cha Inhambane, nchokongola kwambiri, mofanana ndi mbali zina zambiri za Afirika. Timabwato tosodzera nsomba tokhala ndi nsalu yochititsa mphepo kukankha timayenda m’mbali mwa nyanja. Mitengo ya mgwalangwa njambiri. Komano mbali ina yowopsa yakantha zigawo zakumidzi: nkhondo yachiŵeniŵeni!
Kwa awo ogona m’tinyumba tofoleredwa ndi makhwatha amigwalangwa m’maola a mbandakucha, sikwachilendo kudzutsidwa ndi kuphulika kwa mabomba a zida zankhondo zazikulu m’midzi yapafupi pamene nkhondo yamtchireyo ikulirima mkati mwa usiku. Kaŵirikaŵiri ziri nzika zopanda liwongo zimene zimavutika. Nthaŵi zina ana amawonedwa akuyenda motsimphina opanda chiŵalo china kapena atathyoledwa. Ngakhale Mboni za Yehova zina ziri ndi zipsera pankhope zawo ndi m’matupi zochititsidwa ndi nkhalwe zimene zakumana nazo.
Pansi pa mikhalidwe imeneyi Msonkhano Wachigwo wakuti “Okonda Ufulu” unayamikiridwa kwambiri ndi onse amene anafikapo. Mosasamala kanthu za kuthekera kwa kuchitiridwa chiŵembu m’njira yomka kumsonkhano wachigawo, timagulu tabanja tambiri tochokera kumadera akumidzi tinali totsimikizira kudza. Kufika kumeneko sikunalinso kosavuta, popeza kuti zoyendera za anthu onse kwakukulukulu ndizo kukwera pamalole opanda denga. Nthaŵi zina apaulendo okwanira 400 amapanikizana m’lole imodzi! Chiŵerengero chingapo cha malole ameneŵa chimayendera pamodzi motsatana ndi galimoto zolonda zamagulu ankhondo.
Nora ndi ana ake aakazi atatu, ausinkhu wa chaka chimodzi, zaka zitatu, ndi zisanu ndi chimodzi, anali limodzi la mabanja amene anaika pachiswe miyoyo yawo mwa kuyenda ulendo mwanjira imeneyi. Iye anali atasunga ndalama kwamiyezi yambiri pasadakhale kuti adzathe kulipirira ulendowo. Chenicheni chakuti panalibe malo ogona otsimikizirika pamsonkhano wachigawowo sichinamtayitse mtima. Limodzi ndi ena ambiri, Nora ndi banja lake ankangophika chakudya, kudya, ndi kugona pabwalo losonkhana pomwepo.
Ngakhale kutentha koŵaula kwa malo otentha kotsatiridwa ndi kuvumba kwa mvula yochititsa liyambwe sizinazimiriritse chikondwerero chachikulucho cha abale cha kusangalalira limodzi phwando lauzimu. Iwo analingalira kuti panalibe chofunika koposa kwa iwo koposa kukhala pamsonkhano wachigawo. Anthu okwanira 17 anachitira chisonyezero kudzipereka kwawo m’madzi ofunda a Indian Ocean. Pamene ubatizo unayambika, makamu aakulu a owonerera anasonkhezeredwa kuimbira Yehova zitamando.
Kagulu kameneka ka olambira kanalidi katatulukira chimene kukhala okonda ufulu wa Mulungu kumatanthauza. Hans, woimira wa kumalikulu a dzikolo, Maputo, ananena kuti: “Tangowona chiyambi chabe cha nyengo yatsopano ina m’ntchito ya Mboni za Yehova kumbali ino ya Afirika.”