Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 9/1 tsamba 32
  • Kututa kwa Mlaliki Wowona

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kututa kwa Mlaliki Wowona
  • Nsanja ya Olonda—1992
Nsanja ya Olonda—1992
w92 9/1 tsamba 32

Kututa kwa Mlaliki Wowona

WILLIAM R. BROWN choyamba anapita ku Afirika mu 1923. Iye limodzi ndi mkazi wake ndi mwana, ‘anachita ntchito yamlaliki’ mu The Gambia, Ghana, Liberia, Nigeria, ndi Sierra Leone. (2 Timoteo 4:5) Zipatso za ntchito yake nzapadera.

Nzika ya ku West Indies imeneyi sinali chimodzi cha ziŵalo za matchalitchi a Chikristu Chadziko ndipo ndithudi sinaphatikizidwe m’ndale za dziko. Mmalomwake, iye anatsanzira Yesu ndi atumwi mwa kulengeza dzina ndi uchifumu wa Yehova, akumagogomezera kufunika kwa dipo, ndi kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu. (Mateyu 9:35; 20:28; Yohane 17:4-6) William R. Brown mosalekeza anagwiritsira ntchito Baibulo, akumalisonyeza kukhala ukumu wotsiriza m’nkhani za chiphunzitso ndi chikhulupiriro. (2 Timoteo 3:16) Iye anali wakhama kwambiri pazimenezi kwakuti anadziŵidwa monga Bible Brown.

Pokhala ndi dalitso la Yehova, mbewu zimene zinafesedwa ndi Bible Brown zinaphuka ndi kukula. Lerolino, m’maiko amene iye analambula njira, pafupifupi anthu a mu Afirika 200,000 apatulira miyoyo yawo kwa Mlengi ndipo, nawonso, amalalikira mbiri yabwino Yaufumu kwa ena. (Mateyu 24:14; 1 Akorinto 3:6-9) Akristu okangalika ameneŵa amadziŵika ponseponse ndi kuwona mtima kwawo ndi kudalirika. Iwo amanyadira kukhala Mboni za Yehova ndi ogonjera kwa Kristu, Mfumu yolamulirayo.

Kututa kotero ndiko chotulukapo cha ulaliki Wachikristu chowona. Kututa kofananako kukuchitika kuzungulira padziko lonse pakontinenti iriyonse yokhalidwa ndi anthu. M’maiko oposa 200, amuna ndi akazi a mitima yofatsa oposa mamiliyoni anayi ‘atutidwa’ ndipo akubwereza kunena mawu a mngelo wolalikirayo kwa ena kuti: “Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake.” (Chivumbulutso 14:7) Kunena zowona, njira yokha yopezera chiyembekezo m’nyengo yathu ya mavutoyi ndiyo kutembenukira kwa Mulungu ndi kudzigonjetsera kuulamuliro wa Ufumu wake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena