Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 10/15 tsamba 32
  • Ulosi Ukwaniritsidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ulosi Ukwaniritsidwa
  • Nsanja ya Olonda—1992
Nsanja ya Olonda—1992
w92 10/15 tsamba 32

Ulosi Ukwaniritsidwa

PAMENE Kristu Yesu anafunsidwa ndi ophunzira ake za chizindikiro cha kukhalapo kwake kosawoneka mumphamvu ya Ufumu, Yesu ananeneratu za “kuchuluka kwa kusayeruzika.” (Mateyu 24:3, 12) Kodi ulosiwu ukukwaniritsidwa m’nthaŵi yathu?

Ndithudi ukutero! Bukhu lakuti The United Nations and Crime Prevention, lofalitsidwa ndi UN mu October 1991, likuti: “Upandu waukulu ndiwo vuto limodzi lalikulu koposa kumitundu yambiri ya dzikoli. Upandu wa mkati mwa dziko waposa mphamvu ya kuuletsa ya maiko ochuluka ndipo upandu wochitidwira m’dziko la eni wawonjezereka kwakuti sungaletsedwe ndi chitaganya cha maiko onse. . . . Upandu wolinganizidwa ndi timagulu ta apandu wawonjezereka kufikira pamilingo yowopsa, wokhala ndi zotulukapo zowopsa ponena za chiwawa chenicheni, chiwopsezo ndi psete la akuluakulu a boma. Uchigaŵenga wapha anthu osalakwa zikwi makumi ambiri. Kugwiritsira ntchito anthu ena kuchita malonda a mankhwala oledzeretsa kwakhala tsoka lapadziko lonse. Kuwononga dala mwaupandu malo okhala kukuchitika m’mipangidwe yowopsa ndi yaikulu kwakuti kwazindikiridwa kukhala upandu wochitira dziko lenilenilo.”

Kuukira: Kunawonjezeka kuchokera pakuukira 150 pa anthu 100,000 mu 1970 kufikira pafupifupi pakuukira 400 pa anthu 100,000 mu 1990.

Umbala: Unawonjezeka kuchokera kuposa pang’ono 1,000 pa anthu 100,000 mu 1970 kufikira pa 3,500 pa anthu 100,000 mu 1990.

Kuchita Mbanda Kwapadziko lonse: M’maiko osatukuka, kunawonjezeka kuchokera pa 1 kufikira pa 2.5 pa anthu 100,000 pakati pa 1975 ndi 1985. M’maiko otukuka kale chiwonjezeko cha nyengo yofananayo chinapitirira pang’ono pa 3 kufikira pa 3.5.

Maupandu okhudza mankhwala oledzeretsa: Bukhulo limati: “Mabizinesi akuluakulu ogulitsa mankhwala oledzeretsa ali ndi ndalama ndi mfuti zambiri kuposa Maboma a maiko aang’ono, ndipo kufikira pano akhoza kulepheretsa zoyesayesa za kuika chiletso ndi malamulo a maiko okhuphuka.”

Mlingo wonse wa upandu: Ukuyembekezeredwa kuŵirikiza kaŵiri kuyambira pa maupandu 4,000 pa anthu 100,000 mu 1985 kukafika pafupifupi maupandu 8,000 m’chaka cha 2000.

Kuwonjezereka kwapadziko lonse muupandu kuli mbali imodzi yokha ya ulosi wa Yesu wosonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza a dongosolo la zinthu.’ (Mateyu 24:3) Yesu anati: “Pakuwona zinthu izi zirikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.”​—Luka 21:31.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena