“Mboni Yokhulupirika Kuthambo”
KUYAMBIRA kalekale munthu woyamba asanakhale padziko lapansi, mwezi waunikira moŵala m’mlengalenga usiku. Panthaŵi ina ambiri anaulambira monga mulungu wachikazi. Wolemba wina Wachigiriki Plutarch ananena kuti mwezi unali malo amene potsirizira pake miyoyo yangwiro inali kupitako pambuyo pa imfa. M’nthanthi Zachibaltic mwezi unali wamphongo, mwamuna wa dzuŵa. Izo zinali ndi mkangano mu ukwati, ndipo mwezi unathaŵa mkazi wake, amene samawonekera kaŵirikaŵiri limodzi naye m’miyambamo!
Lerolino, okondana—achichepere ndi achikulire omwe—amatukulira mitu yawo kumwezi nakhala ndi maganizo akukondana. M’ma 1960 asayansi anathera ndalama zambirimbiri kupititsa anthu pa mwezi ndi kubwera ndi miyala yolemera mapaundi angapo kuti adzafufuze. Chinthu chimodzi ponena za mwezi chiri chotsimikizirika. Tsiku lirilonse, panthaŵi yolinganizidwa yeniyeni, udzatuluka ndi kuloŵa. Ngwokhulupirika kwambiri m’maulendo ake ozungulira kotero kuti tingathe kuŵerengera kuwonekera kwake ndi kudetsedwa kwake zaka zikwi zambirimbiri pasadakhale.
Pamene Aisrayeli anayang’ana mwezi, anakumbutsidwa za kanthu kena kodabwitsa. Mulungu analonjeza kuti mzera wachifumu wa Mfumu Davide sukachoka konse. Iye anati: ‘Mofanana ndi mwezi [mbewu ya Davide] idzakhazikika zolimba kunthaŵi yosadziŵika, ndi ngati mboni yokhulupirika kuthambo.’ (Salmo 89:35-37) Lonjezo limeneli linakwaniritsidwa mwa Yesu, “Mwana wa Davide.” (Luka 18:38) Pambuyo pa imfa yake Yesu anaukitsidwa monga mzimu wosakhoza kufa ndipo anakwera kumwamba. (Machitidwe 2:34-36) M’kupita kwanthaŵi anaikidwa pampando wachifumu monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu. (Chivumbulutso 12:10) Ufumuwo tsopano ukulamulira ndipo “udzakhala kosatha.” (Danieli 2:44) Mwanjirayi, Yesu woimira wosakhoza kufa wa mzera Wachifumu wa Davide, adzakhala kwautali wonga mwezi, monga “mboni yokhulupirika kuthambo.”
Chotero, nthaŵi iriyonse pamene muwona mwezi ukuunikira moŵala m’thambo usiku, kumbukirani lonjezo la Mulungu kwa Davide ndipo perekani zithokozo kuti Ufumu wa Mulungu tsopano ukulamulira ndipo udzalamulira kosatha, ku ulemerero wa Mulungu ndi dalitso losatha kwa anthu okhulupirika.—Chivumbulutso 11:15.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
Frank Zullo