Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 3/15 tsamba 31-32
  • Kufupidwa ndi “Kolona wa Moyo”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufupidwa ndi “Kolona wa Moyo”
  • Nsanja ya Olonda—1993
Nsanja ya Olonda—1993
w93 3/15 tsamba 31-32

Kufupidwa ndi “Kolona wa Moyo”

MTUMWI Yohane anauzidwa kulembera mngelo wa mpingo wa ku Smurna kuti: “Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe kolona wa moyo.” (Chivumbulutso 2:8, 10) Chotero, panopa chilengezo chomvetsa chisoni komanso chosangalatsa chikuperekedwa chakuti, Frederick William Franz, pulezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., kuphatikizapo mabungwe ena angapo ateokratiki, anamaliza moyo wake wapadziko lapansi pa December 22, 1992 m’maŵa.

Nchilengezo chomvetsa chisoni mwanjira yakuti chimatiuza za kutha kwa ntchito za padziko lapansi za mtumiki wa Yehova wokondedwa koposa ndi wokhulupirika mwapadera. Komabe, chirinso chilengezo chosangalatsa chifukwa chakuti, tsopano mawu a pa Chivumbulutso 14:13 akwaniritsidwa kwa Mbale wathu wokondedwa Franz akuti: ‘Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zawo; pakuti ntchito zawo zitsatana nawo pamodzi.’ Mbale Franz anali wodekha ndi wodzichepetsa, mtumiki wogwira ntchito mwamphamvu ndi wotulutsa zipatso kwambiri amene Yehova Mulungu anamgwiritsira ntchito m’zinthu zazikulu monga chiŵalo cha “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuthandizira m’kugaŵira “banja” ndi atsamwali awo chakudya chauzimu.​—Mateyu 24:45-47.

Mbale Franz anabadwa pa September 12, 1893, mu Covington, Kentucky. Iye anamva chowonadi kupyolera mwa mchimwene wake wamkulu. Panthaŵiyo, iye anali kuchita maphunziro pa Yunivesite ya Cincinnati, akukonzekera kudzakhala minisitala wa Tchalitchi cha Presbyterian. Mmalo mwake, iye analekana ndi Tchalitchi cha Presbyterian nagwirizana ndi Ophunzira Baibulo, dzina limene Mboni za Yehova zinatchedwa nalo panthaŵiyo. Anabatizidwa pa November 30, 1913, ndipo chaka chotsatira anachoka pa Yunivesite ndi kuyamba ntchito ya ukopotala (upainiya). Pa June 1, 1920, anakhala chiŵalo cha banja la Betele ya Brooklyn. Posapita nthaŵi, anaikidwa kukhala woyang’anira ntchito yosamalira za ukopotala, ndipo mu 1926 anasamutsidwira ku dipatimenti yokonza nkhani, kumene anatumikira kwambiri. Mu 1945 anakhala wachiŵiri kwa pulezidenti wa Watch Tower Society ndi mabungwe ake ena. Pamene pulezidenti wapanthaŵiyo Nathan H. Knorr anamwalira mu 1977, iye anakhala pulezidenti wa Watch Tower Society. Anatumikira paudindo umenewo kufikira imfa yake. M’moyo wake, Mbale Franz anawona chiŵerengero cha Mboni za Yehova chikuwonjezereka kuchokera pa zikwi zoŵerengeka kufikira pafupifupi mamiliyoni anayi ndi theka. Iye anasangalala ndi mwaŵi wosiyanasiyana wa mautumiki, kuphatikizapo kulankhula pa misonkhano ya mitundu yonse ndi kuchezera nthambi ndi nyumba za amishonale m’mbali zosiyanasiyana za dziko. Mbiri ya moyo wake inatuluka m’kope la Nsanja ya Olonda ya May 1, 1987.

Pa Lolemba madzulo, December 28, 1992, programu ya maliro ake inachitidwa m’Nyumba Yaufumu pa Betele ya Brooklyn. Nkhani yothutsa mtima ndi yolimbikitsa kwambiri mwauzimu inakambidwa ndi Mbale Albert D. Schroeder wa Bungwe Lolamulira. Mabanja a Betele a ku Watchtower Farms, Patterson, Mountain Farm, ndi Kingdom Farm, limodzi ndi banja la Betele ku nthambi ya Canada onse analunzanitsidwa ndi foni.

Onse, makamaka awo amene anagwira ntchito pamodzi naye, adzamlakalaka kwambiri Mbale Franz. Iye anali wokoma mtima, wolimbikitsa, ndi woleza mtima kwa aliyense amene anatumikira ndi kuyenda naye. Kunena zowona, okhulupirira anzake anachita naye mogwirizana ndi Ahebri 13:7: ‘Kumbukirani atsogoleri anu, amene analankhula nanu mawu a Mulungu; ndipo poyang’anira chitsirizo cha mayendedwe awo mutsanze chikhulupiriro chawo.’

Pa December 30, 1992, Mbale Milton G. Henschel anasankhidwa monga Pulezidenti wachisanu wa Sosaite kuloŵa m’malo Mbale Franz.

[Zithunzi pamasamba 31, 32]

Frederick W. Franz mu 1913

Pa fekitale ya Sosaite la m’khwalala Myrtle Avenue mu 1920

Ali ndi Nathan H. Knorr pa Yankee Stadium mu 1953

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena