Chochitika Chofunika Koposa m’Mbiri
Kodi nchifukwa ninji chili chotero? Chochitikacho chinali imfa ya Yesu Kristu.
Chinachititsa kulemekezedwa kwa uchifumu wa Mulungu ndi kutsimikizira kuti munthu akhoza kusunga umphumphu wokwanira kwa Mulungu. Chinapereka kwa anthu chiyembekezo chakupeza moyo wosatha m’mikhalidwe yaparadaiso. Yesu mwiniyo anayambitsa chikumbutso cha imfa yake usiku asanafe.
Chinali dzoma losacholoŵana. Padzomalo, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Chitani ichi chikumbukiro changa.” (Luka 22:19, 20) Kodi mudzakumbukira? Mboni za Yehova zikukuitanani kugwirizana nazo kuchita phwando limeneli lofunika koposa m’mbiri. Chaka chino lidzakhalako pa Lachiŵiri, April 6, dzuŵa litaloŵa.
Chonde funsani pa Nyumba Yaufumu yapafupi nanu ponena za nthaŵi yeniyeni ndi malo. Palibe zopereka zimene zidzatengedwa, ndipo alendo akuitanidwa kudzamvetsera nkhani yophunzitsa ndi kuwona zochitika zosavuta.