Ndodo Yachifumu ya Makangaza ya m’Nyumba ya Yehova?
OFUKULA za m’mabwinja m’Israyeli afukula ndodo zachifumu zambiri, ndodo zonyamulidwa ndi anthu aukumu. (Genesis 49:10; Estere 8:4; Ezekieli 19:14) Ndodo zachifumu zina zopezeka m’Lakisi zinali ndi mutu wonga ngati makangaza. Anthu a Mulungu anadziŵa chipatso chimenechi bwino lomwe.—Deuteronomo 8:8; Nyimbo ya Solomo 4:13.
Mnyanga wonga makangaza ongoyamba kuphukira womwe uli kulamanzerewu, unatulukiridwa osati kale kwambiri. Ngwamsinkhu wa mamilimita 43, ndipo chiboo cha patsinde pake chikusonyeza kuti unali mbali ya ndodo yachifumu. Tawonani zilembo zozokotedwa mumpangidwe wa Chihebri choyambirira cha m’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E.
Mbali yamnyangawo inasweka m’nthaŵi zakale, chotero zilembo zoŵerengeka palibe kapena zikuwonekera pang’ono. Komabe, akatswiri odziŵa malembedwe amakedzana akunena kuti cholembedwa m’munsi panopa ndicho chobwezeretsedwa chake. (Chozikidwa pa Biblical Archaeologist) Mipata yosalingana ya pakati pa zilembo yachititsa kuŵerenga kuŵiri kwakukulu. Katswiri Wachifalansa André Lemaire anapereka kuŵerenga kwakuti “Ya m’Ka[chisi wa A[mbu]ye [Yahweh], yopatulika kwa ansembe.” Nahman Avigad anati “Chopereka chopatulika cha ansembe a (mu) Nyumba ya Yahweh.”
Iwo ndi akatswiri ena ananena kuti ndodo yachifumuyo poyamba inali ndi zilembo zinayi Zachihebri za dzina laumwini la Mulungu—Yehova. Chotero ikanatchula “nyumba ya Yehova,” mawu ofala m’Baibulo.—Eksodo 23:19; 1 Mafumu 8:10, 11.
Ambiri amalingalirabe kuti mutu wandodo yachifumu imeneyi ungakhale unali wa ansembe pakachisi amene Solomo anamanga kapena kuti unaperekedwa monga chopereka kukachisi ameneyo. Mokondweretsa, mpangidwe wa makangaza unali kuwonedwa kaŵirikaŵiri m’kachisi wa Mulungu.—Eksodo 28:31-35; 1 Mafumu 7:15-20.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32
Israel Museum, Jerusalem