Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Pa Aroma 9:3, mtumwi Paulo analemba kuti: “Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Kristu chifukwa cha abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi.” Kodi iye anatanthauza kuti akapereka moyo wake kuti apulumutse Ayuda anzake?
Yesu anapereka chitsanzo chopambana cha chikondi. Iye anali wofunitsitsa kupereka moyo wake kaamba ka mtundu wa anthu ochimwa. Muutumiki wake wapoyera, anagwira ntchito zolimba chifukwa cha anthu a dziko lake—Ayuda—kotero kuti ochuluka monga momwe kukanathekera akakhale pakati pa awo amene akapindula ndi nsembe yake ya dipo. (Marko 6:30-34) Kusalabadira kwawo ndi kutsutsa kwawo uthenga wa chipulumutso sikunafooketse nkhaŵa yachikondi ya Yesu pa anthu Achiyuda. (Mateyu 23:37) Ndipo iye anasiya ‘chitsanzo chakuti tilondole mapazi ake.’—1 Petro 2:21.
Kodi nkotheka kwa anthu opanda ungwiro kutsatira chitsanzo cha Yesu cha chikondi? Inde, ndipo tikhoza kuona chitsanzo cha zimenezi mwa mtumwi Paulo. Iye anali wodera nkhaŵa kwambiri ponena za Ayuda anzake moti, chifukwa cha chikondi chake pa iwo, anati akakhumba iye mwini ‘kuchotsedwa kwa Kristu monga wotembereredwa’ chifukwa cha iwo.
Paulo pamenepo anagwiritsira ntchito mawu osinjirira, kapena okukumaza, kuti amveketse mfundo yake. Yesu anagwiritsira ntchito mawu okukumaza ofananawo pa Mateyu 5:18, pamene anati: “Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang’ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse.” Yesu anadziŵa kuti thambo ndi dziko lapansi sizikachoka. Nayenso Paulo anadziŵa kuti sakatembereredwa, ndi kuti si Ayuda onse amene akalandira Chikristu. Koma mfundo ya Paulo inali yakuti anali wokonzekera kuchita kalikonse kuti athandize Ayuda kupindula ndi makonzedwe a Mulungu a chipulumutso kupyolera mwa Yesu Kristu. Nchifukwa chake mtumwiyo anakhoza kulimbikitsa Akristu anzake kuti: “Khalani onditsanza ine, monga inenso nditsanza Kristu”!—1 Akorinto 11:1.
Lerolino, Akristu ayenera kukhala ndi nkhaŵa yofanana ndi imene Yesu ndi Paulo anali nayo kaamba ka osakhulupirira. Sitiyenera konse kulola mphwayi kapena chitsutso cha anthu a m’gawo lathu lolalikiramo kufooketsa chikondi chathu pa anansi athu ndi changu chathu cha kuwathandiza kuphunzira njira ya chipulumutso.—Mateyu 22:39.