Mofanana ndi Mtengo
“NDAKATULO zimapangidwa ndi zitsiru zonga ine, koma Mulungu yekha ndiye angapande mtengo.” Pothokoza maubwino ambiri a mitengo, wolemba ndakatulo Joyce Kilmer analemekeza Mulungu motero pokhala ndiye anailenga.
Yehova Mulungu anapanga mitengo yambiri yamitundumitundu, yokongoletsa, ndi yogwiritsira ntchito. Yaing’ono ndi yaikulu yomwe, ingakhale yokongola kwambiri kwakuti mawu okha sangathe kuilongosola. Ndiponso, mitengo imapereka chakudya, nkhuni, ndi mthunzi. Ndipo amisiri akupitirizabe kupeza njira zatsopano zogwiritsirira ntchito mitengo.
M’Baibulo, mitengo nthaŵi zina imagwiritsiridwa ntchito mophiphiritsira kuimira maufumu, olamulira, ndi anthu ena. (Ezekieli 31:1-18; Danieli 4:10-26) Mitengo imatchulidwa mogwirizanitsidwa ndi chimwemwe, mtendere, ndi mikhalidwe yopindulitsa yochokera muulamuliro wa Yehova ndi kubwezeretsedwa kwa anthu ake. (1 Mbiri 16:33; Yesaya 55:12; Ezekieli 34:27; 36:30) Malemba amalonjezanso kuti masiku a anthu a Mulungu adzakhala monga a mtengo. (Yesaya 65:22) Zimenezi zili ndi tanthauzo lalikulu pamene tizindikira kuti mitengo ina imakhala kwa zaka mazana ambiri.
Wamasalmo wa m’Baibulo ananena kuti munthu amene amakondwera ndi chilamulo cha Mulungu “akunga mtengo wooka pamitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake panyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.” Mtengo wokondwa wookedwa m’mphepete mwa madzi ambiri unakumbutsa wamasalmoyo za ulemerero wauzimu umene awo ‘okondwera m’chilamulo cha Yehova,’ amasangalala nawo. (Salmo 1:1-3) Ngati mukhala ndi chisangalalo chenicheni m’chilamulo cha Mulungu ndi Mawu Opatulika, masiku anu angakhale onga a mtengo. Kwenikweni, mwakuchita mogwirizana ndi chidziŵitso cholongosoka chonena za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu, mukhoza kusangalala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.—Yohane 17:3.