Kodi Angakupindulitseni?
MAGAZINI amene muli nawo m’manja mwanu alinganizidwa kukhala magwero a chilimbikitso, akumakumbutsa zitsogozo Zabaibulo zochititsira mabanja kukhala okhazikika ndi kusunga umphumphu wa munthu mwini. Amasonyeza kuti nthaŵi ya mavuto ya lerolino inanenedweratu m’Baibulo, ndipo amagogomezera mankhwala ake—boma la Ufumu wa Mulungu. Kodi mungapindule ndi Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, magazini anzake?
Kuchokera ku Philippines mkazi wina wotchedwa Vilma analemba kuti: “Ngati pakanakhala mawu ena ofotokozera magazini anu, ndikanasankha akuti ‘abwino koposa.’ Ndinaona ndi kuŵerenga kwanthaŵi yoyamba Galamukani! wanu ndi Nsanja ya Olonda pamene ndinali m’basi pobwerera kwathu kuchokera ku Manila. Kaŵirikaŵiri ndimanyamula nyuzipepala pamene ndili paulendo, koma panthaŵiyi ndinalibe.
“Amene anakhala nane pafupi anali mwamuna wina wa zaka zapakati amene anali ndi magazini anu. Pamene anamaliza kuŵerenga Galamukani!, anatulutsanso magazini ena, Nsanja ya Olonda. Ndinagwiritsira ntchito mpatawo kubwereka Galamukani! Kunena zowona, ndinakondwera kuŵerenga magazini amenewo chifukwa chakuti nkhani zake zinali zokondweretsa, zapanthaŵi yake, ndi zotsitsimula.”
Ndiyeno mkaziyo anamaliza kuti: “Ndikufuna kumalandira magazini anu. Chonde tandiuzani mmene ndingamawalandirire.” Ofesi yanthambi ya Mboni za Yehova ku Philippines inali yachimwemwe kuchita mogwirizana ndi zimenezi mwa kuwonjezera mkazi ameneyu pampambo wawo wa positi.